LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb20 October tsa. 4
  • Makhalidwe Abwino a Yehova

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Makhalidwe Abwino a Yehova
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2020
  • Nkhani Zofanana
  • Kodi Cikondi Cosasintha ca Yehova N’ciani?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2021
  • “Cikondi Sicitha”
    ‘Imbani Mokweza ndi Mosangalala’ kwa Yehova
  • Cikondi Cokhulupilika Cimam’kondweletsa Yehova—Nanga Imwe?
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano —2017
  • Kodi Yehova ni Mulungu Wotani?
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2020
mwb20 October tsa. 4

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKSODO 33-34

Makhalidwe Abwino a Yehova

34:5-7

Mose anali kuwadziŵa bwino makhalidwe a Yehova. Izi zinam’thandiza kuti azicita zinthu moleza mtima na Aisiraeli. Na ife ngati tiyesetsa kuwadziŵa bwino makhalidwe a Yehova, tidzakwanitsa kucita zinthu mwacifundo na Akhristu anzathu.

  • “Wacifundo ndi wacisomo”: Yehova amasamalila olambila ake mwacikondi kwambili ndiponso amawadela nkhawa kwambili, monga mmene makolo amasamalila ana awo

  • “Wosakwiya msanga”: Yehova ni woleza mtima na atumiki ake. Amawalezela mtima akaphonya zinthu zina, ndipo amawapatsa mpata wosintha zophophonya zawo

  • “Wodzaza ndi kukoma mtima kosatha”: Cikondi ca Yehova pa anthu ake n’cosatha. Conco ubwenzi wawo na iye sudzatha

Zithunzi: Mboni za Yehova zikutengela makhalidwe a Yehova. 1. Akulu aŵili akucita ulendo waubusa ku banja lina, ndipo akupeleka cilimbikitso ca m’Baibo. 2. Mlongo akutonthoza mlongo mnzake amene akulila.

DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi ningatengele bwanji khalidwe la Yehova la cifundo?’

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani