UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Acinyamata—Kodi Yehova ni Bwenzi Lanu Lapamtima?
Kodi ni munthu wa makhalidwe otani amene mumafuna atakhala mnzanu? Mwacionekele mumafuna atakhala wokhulupilika, wokoma mtima, komanso wowoloŵa manja. Yehova ali nawo makhalidwe onse amenewa. (Eks. 34:6; Mac. 14:17) Mulungu amamvetsela mukamapemphela kwa iye. Amakuthandizani mukafunika thandizo. (Sal. 18:19, 35) Amakukhululukilani mukalakwa. (1 Yoh. 1:9) Ndithudi, Yehova ni Bwenzi labwino ngako!
Kodi mungacite ciani kuti mukhale bwenzi la Yehova? Phunzilani za iye mwa kuŵelenga Mawu ake. Muuzeni za mumtima mwanu komanso nkhawa zanu. (Sal. 62:8; 142:2) Onetsani kuti mumakonda zinthu zimene Yehova amaona kuti n’zofunika. Zinthu monga Mwana wake, Ufumu wake, komanso malonjezo ake. Muziuzako ena za Mulungu. (Deut. 32:3) Mukapanga ubwenzi wolimba na Yehova, iye adzakhala Bwenzi lanu kwamuyaya.—Sal. 73:25, 26, 28.
TAMBANI VIDIYO YAKUTI ACINYAMATA—“TALAWANI NDIPO MUONE KUTI YEHOVA NDI WABWINO,” NDIPO PAMBUYO PAKE YANKHANI MAFUNSO AWA:
Mungakonzekele bwanji kudzipatulila kwa Mulungu na ubatizo?
Kodi ena mumpingo angakuthandizeni bwanji kutumikila Yehova?
Kodi kulalikila kungalimbitse bwanji ubale wanu na Yehova?
Mungathe kukhala pa ubwenzi na Yehova kwamuyaya!
Ni mautumiki ati m’gulu la Mulungu amene mungaciteko?
N’ciani cimene mumakonda kwambili ponena za Yehova?