December 14-20
LEVITIKO 12-13
Nyimbo 140 na Pemphelo
Mawu Oyamba (1 min.)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Phunzilamponi Kanthu pa Malamulo Okhudza Nthenda ya Khate”: (10 min.)
Lev. 13:4, 5—Anthu odwala khate anali kuwaika kwaokha (wp18.1 7)
Lev. 13:45, 46—Anthu akhate anali kufunika kupewa kufalitsa matendawo kwa ena (wp16.4 9 ¶1)
Lev. 13:52, 57—Zinthu zimene pafalikila matendawa zinali kuwonongedwa (it-2 238 ¶3)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (10 min.)
Lev. 12:2, 5—N’cifukwa ciani mkazi anali kukhala “wodetsedwa” akabeleka mwana? (w04 5/15 23 ¶2)
Lev 12:3—Kodi mwina n’cifukwa ciani Yehova analamula kuti ana azidulidwa pa tsiku la 8? (wp18.1 7)
Pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino, ni mfundo yopindulitsa iti imene munapeza yokhudza Yehova, ulaliki, kapena mfundo ina iliyonse?
Kuŵelenga Baibo: (4 min. olo kucepelapo) Lev. 13:9-28 (th phunzilo 5)
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Vidiyo ya Ulendo Wobwelelako: (4 min.) Kukambilana. Tambitsani vidiyo imeneyi. Ndiyeno funsani omvetsela mafunso awa: Kodi Tony waseŵenzetsa bwanji mafunso mwaluso? Nanga wam’thandiza bwanji mwininyumba kudziŵa bwino moseŵenzetsela mfundo ya pa lemba?
Ulendo Wobwelelako: (4 min. olo kucepelapo) Mukayamba makambilano acitsanzo, mwininyumba akambe mawu ofala kwanuko ofuna kukanila ulaliki. Koma mwaluso, loŵelani pa mawu amenewo. (th phunzilo 19)
Ulendo Wobwelelako: (5 min. olo kucepelapo) Yambani na makambilano acitsanzo. Gaŵilani bulosha yakuti Uthenga Wabwino na kuyambitsa phunzilo la Baibo pa phunzilo 11. (th phunzilo 9)
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Zofunikila za Mpingo: (15 min.)
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min. olo kucepelapo) lfb phunzilo 9, 10
Mawu Othela (3 min. olo kucepelapo)
Nyimbo 36 na Pemphelo