CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | LEVITIKO 12-13
Phunzilamponi Kanthu pa Malamulo Okhudza Nthenda ya Khate
13:4, 5, 45, 46, 52, 57
Kodi mfundo zimene panazikidwa malamulo okhudza nthenda ya khate zitiphunzitsa ciani pa nkhani yoteteza umoyo wathu wauzimu?
Yehova anaphunzitsa ansembe mmene angaidziŵile mwamsanga nthenda ya khate. Abusa acikhristu masiku ano amacita cangu kuthandiza anthu amene afunika thandizo lauzimu.—Yak. 5:14, 15
Aisiraeli anali kuwononga cinthu ciliconse cimene khate lafalikilapo, pofuna kuti lisapitilize kufalikila. Nawonso Akhristu afunika kulolela kuleka kapena kudzimana zinthu zina m’malo molola kuti zinthuzo ziwagwetsele m’chimo. (Mat. 18:8, 9) Zinthu zimenezo zingaphatikizepo zizoloŵezi zoipa, mayanjano, kapena zosangalatsa zoipa
Kodi munthu angaonetse bwanji kuti afunitsitsa kulandila thandizo locokela kwa Yehova?