LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb21 July tsa. 5
  • “Musamade Nkhawa”

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • “Musamade Nkhawa”
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
  • Nkhani Zofanana
  • Zikumbutso za Msonkhano Wacigawo
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Msonkhano (2016)
  • Kodi Baibo Imakamba Ciyani pa Zanchito Komanso Ndalama?
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
mwb21 July tsa. 5
Banja losauka la anthu 6 likuyenda m’dela la anthu osauka popita kukasonkhana na abale awo.

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

“Musamade Nkhawa”

Yehova anali kuthandiza anthu osauka mu Isiraeli wakale. Kodi n’ziti zina zimene wacita pothandiza atumiki ake osauka masiku ano?

  • Anawaphunzitsa kuona ndalama moyenela.—Luka 12:15; 1 Tim. 6:6-8

  • Amawathandiza kudziona kuti ni ofunika.—Yobu 34:19

  • Anawaphunzitsa kugwila nchito molimbika na kupewa zizoloŵezi zoipa.—Miy. 14:23; 20:1; 2 Akor. 7:1

  • Anawabweletsa m’gulu lacikondi la abale acikhristu.—Yoh. 13:35; 1 Yoh. 3:17, 18

  • Anawapatsa ciyembekezo.—Sal. 9:18; Yes. 65:21-23

Olo zinthu zivute bwanji pa umoyo, sitiyenela kuda nkhawa. (Yes. 30:15) Yehova adzatithandiza kupeza zofunikila zakuthupi, malinga ngati tipitiliza kufuna-funa ufumu wake coyamba.—Mat. 6:31-33.

ONELELANI VIDIYO YAKUTI CIKONDI SICITHA OLO KUTI. . . NDIMWE OSAUKA​—CONGO, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AWA:

  • Cithunzi coonetsa zocitika za mu vidiyo yakuti ‘Cikondi Sicitha Olo Kuti . . . Ndimwe Osauka—Congo.’ Gulu la abale na alongo liyenda ku malo a msonkhano wacigawo. Ambili anyamula mipando na zinthu zina.

    Kodi abale amene amakhala kufupi na malo ocitilako msonkhano wacigawo, amaonetsa bwanji mzimu woceleza kwa abale ocokela kutali obwela ku msonkhano?

  • Cithunzi coonetsa zocitika za mu vidiyo yakuti ‘Cikondi Sicitha Olo Kuti . . . Ndimwe Osauka—Congo.’ M’bale akonza bedi m’nyumba yake kuti abale ocokela kutali agonepo.

    Kodi vidiyo imeneyi itiphunzitsa ciani za cikondi ca Yehova pa osauka?

  • Cithunzi coonetsa zocitika za mu vidiyo yakuti ‘Cikondi Sicitha Olo Kuti . . . Ndimwe Osauka—Congo.’ Abale akuvala kuti akapezeke pa msonkhano wacigawo.

    Kaya ndife olemela kapena osauka, tingatengele bwanji citsanzo ca Yehova?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani