LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb23 January tsa. 5
  • Limbitsani Cikhulupililo Canu pa Mawu a Mulungu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Limbitsani Cikhulupililo Canu pa Mawu a Mulungu
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
  • Nkhani Zofanana
  • Zisankho Zimene Zimaonetsa Kuti Timadalila Yehova
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
  • Kufuna-funa Nzelu mwa Kuŵelenga Baibo Tsiku Lililonse
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
  • Pezani Mayankho pa Mafunso Aya
    2025-2026 Pulogilamu ya Msonkhano wa Dela—Wa Woyang’anila Dela
  • Pezani Mayankho pa Mafunso Aya
    2025-2026 Pulogilamu ya Msonkhano wa Dela—Wa Woimila Nthambi
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
mwb23 January tsa. 5
Zithunzi: Mlongo wacitsikana akuphunzila Baibo. 1. Walemba chati yoonetsa nthawi imene anthu ochulidwa m’Baibo anakhalako. 2. Akuŵelenga “Baibulo la Dziko Latsopano” Lophunzilila pa jw.org. 3. Akufufuza pa mapu oonetsa malo ochulidwa m’Baibo. 4. Wajambula cithunzi ca mkulu wa ansembe na kulemba maina a zovala zake.

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Limbitsani Cikhulupililo Canu pa Mawu a Mulungu

Mawu a Mulungu angasinthe umoyo wathu. (Aheb. 4:12) Komabe, kuti tipindule na malangizo ake komanso uphungu wake, tiyenela kukhutila kuti Baibo ni ‘mawudi a Mulungu.’ (1Tim. 2:13) Kodi tingacite ciyani kuti tiziikhulupilila kwambili Baibo?

Muziiŵelenga tsiku lililonse. Pamene muŵelenga, yesetsani kupeza umboni wakuti Yehova ndiye Mlembi wake. Mwacitsanzo, ganizilani malangizo anzelu opezeka m’buku la Miyambo, na kuona mmene amatithandizila pa umoyo wathu masiku ano.—Miy. 13:20; 14:30.

Muzisankha nkhani na kuiphunzila mozama. Dziŵani bwino umboni woonetsa kuti Baibo ni youzilidwadi. Mu Buku Lofufuzila Nkhani la Mboni za Yehova, onani pa mutu wakuti “Baibo,” kenako pa “Inauzilidwa na Mulungu.” Mungalimbitsenso cikhulupililo canu cakuti uthenga wa m’Baibo sunasinthe mwa kuŵelenga nkhani yakuti, “Baibulo Lakumana ndi Zambili” mu Galamukani ya November 2007.

ONELELANI VIDIYO YAKUTI CIFUKWA CAKE TIMAKHULUPILILA . . . MAWU A MULUNGU, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:

  • Kodi cipupa ca kacisi cimene cinapezeka ku Karnak m’dziko la Egypt, cimatsimikizila bwanji kuti Mawu a Mulungu amakamba zoona?

  • Kodi tidziŵa bwanji kuti uthenga wa m’Baibo sunasinthe?

  • Baibo yapulumuka zambili. Kodi izi zimakuthandizani bwanji kutsimikizila kuti Baibo ni mawudi a Mulungu?—Ŵelengani Yesaya 40:8

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani