LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb24 January tsa. 2
  • January 1-7

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • January 1-7
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku Misonkhano—2024
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku Misonkhano—2024
mwb24 January tsa. 2

JANUARY 1-7

YOBU 32-33

Nyimbo 102 na Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Mwa cifundo, Elihu akumvetsela Yobu amene ali na zilonda zoopsa.

Mwa cifundo, Elihu akumvetsela pamene Yobu akufotokoza mmene akumvela

1. Tonthozani Omwe Ali na Nkhawa

(Mph. 10)

Khalani mabwenzi kwa ena (Yobu 33:1; it-1 710)

Khalani acifundo m’malo mowaweluza (Yobu 33:​6, 7; w14 6/15 25 ¶8-10)

Monga Elihu anacitila, yambani mwamvetsela na kuganizilapo musanalakhule (Yobu 33:​8-12, 17; w20.03 23 ¶17-18; onani cithunzi pacikuto)

Mwa cifundo, mlongo akumvetsela mayi wopanikizika maganizo yemwe akulela yekha ana. Ana ake aang’ono aŵili akuseŵela m’cipinda cina.

2. Kufufuza Cuma Cauzimu

(Mph. 10)

  • Yobu 33:25—Kodi vesiyi itithandiza bwanji kusamada nkhawa kwambili na maonekedwe athu tikayamba kukalamba? (w13 1/15 19 ¶10)

  • Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zomwe mungakonde kutigaŵilako?

3. Kuŵelenga Baibo

(Mph. 4) Yobu 32:​1-22 (th phunzilo 12)

CITANI KHAMA PA ULALIKI

4. Kambilanani pa Zokhudza Munthuyo—Mmene Yesu Anacitila Zimenezi

(Mph. 7) Kukambilana. Tambitsani VIDIYO yakuti kenako kambilanani lmd phunzilo 1 mfundo 1-2.

5. Kambilanani pa Zokhudza Munthuyo—Tengelani Yesu

(Mph. 8) Makambilano ozikika pa lmd phunzilo 1 mfundo 3-5 komanso mbali yakuti “Onaninso Malemba Awa.”

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Nyimbo 116

6. Zofunikila za Mpingo

(Mph. 15)

7. Phunzilo la Baibo la Mpingo

(Mph. 30) bt mutu 4 bokosi pa tsa. 30

Mawu Othela (Mph. 3) | Nyimbo 54 na Pemphelo

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani