LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb24 January masa. 3-16
  • January 8-14

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • January 8-14
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku Misonkhano—2024
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku Misonkhano—2024
mwb24 January masa. 3-16

JANUARY 8-14

YOBU 34-35

Nyimbo 30 na Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Ngati Zinthu Sizikukuyendelani pa Umoyo

(Mph. 10)

Kumbukilani kuti Yehova si ndiye amacititsa zopanda cilungamo (Yobu 34:10; wp19.1 8 ¶2)

Zingaoneke ngati anthu ambili salandila cilango pa zoipa zimene amacita, komabe sangathaŵe ciweluzo ca Yehova (Yobu 34:​21-26; w17.04 10 ¶5)

Njila yabwino yothandizila ocitidwa zopanda cilungamo ni kuwaphunzitsa za Yehova (Yobu 35:​9, 10; Mat. 28:​19, 20; w21.05 7 ¶19-20)

Banja la mboni likulalikila mwamuna na mwana wake wamng’ono amene amakhala m’komboni yaing’ono pafupi na zimango zazikulu mu mzinda wotukuka.

2. Kufufuza Cuma Cauzimu

(Mph. 10)

  • Yobu 35:7—Kodi Elihu anatanthauzanji pofunsa Yobu kuti: “Kodi [Mulungu] amalandila ciyani kucokela m’manja mwanu?” (w17.04 29 ¶3)

  • Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zomwe mungakonde kutigaŵilako?

3. Kuŵelenga Baibo

(Mph. 4) Yobu 35:​1-16 (th phunzilo 10)

CITANI KHAMA PA ULALIKI

4. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 3) NYUMBA NA NYUMBA. M’pempheni kuti muyambe kuphunzila naye Baibo. (lmd phunzilo 10 mfundo 3)

5. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 4) ULALIKI WAMWAYI. Onetsani munthu amene ali ni ana aang’ono mmene angapezele nkhani zothandiza makolo pa jw.org. (lmd phunzilo 1 mfundo 4)

6. Kupanga Ophunzila

(Mph. 5) lff phunzilo 13 mfundo 5 (lmd phunzilo 11 mfundo 3)

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Nyimbo 58

7. Kodi Mumalakalaka “Kulalikila Mawu” Mwamwayi?

(Mph. 15) Kukambilana.

Mlongo akuseŵenzetsa foni polalikila mzimayi mu basi.

Paulo analimbikitsa Timoteyo kuti: “Lalikila mawu. Lalikila modzipeleka.” (2 Tim 4:2) Liwu lacigiriki (velebu) lomasulidwa kuti “lalikila modzipeleka,” nthawi zina anali kulichula pokamba za msilikali kapena mlonda amene nthawi zonse anali kukhala cile kuti acitepo kanthu. Mawuwa amafotokoza bwino mmene timakhalila cile nthawi zonse kuti tipeze mpata woloŵetsapo ulaliki pa makambilano.

Cifukwa timamukonda Yehova ndipo timayamikila zonse zimene amaticitila, timafuna kuuzako ena za makhalidwe ake abwino.

Ŵelengani Salimo 71:8. Kenako funsani omvela kuti:

Kodi ni zabwino ziti zokhudza Yehova zimene mumakonda kuuzako ena?

Cikondi cathu pa anthu cimatilimbikitsa kulalikila mwa mwayi.

Tambitsani VIDIYO yakuti Mmene Anthu Ofika M’mahandiledi Anaphunzilila Coonadi. Kenako funsani omvela kuti:

  • Kodi ulaliki wamwayi unathandiza bwanji kuti anthu ofika m’mahandiledi apeze coonadi ca m’Baibo?

  • Kodi anthu omwe poyamba anali acipembedzo cina anapindula bwanji atalandila coonadi?

  • Kodi kukonda anthu kumatilimbikitsa bwanji kucita ulaliki wamwayi?

  • Muona kuti n’cifukwa ciyani ulaliki wamwayi ni njila yabwino kwambili yothandizila anthu kudziŵa Yehova?

8. Phunzilo la Baibo la Mpingo

(Mph. 30) bt mutu 4 bokosi pa tsa. 33

Mawu Othela (Mph. 3) | Nyimbo 138 na Pemphelo

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani