LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb24 January masa. 6-7
  • January 22-28

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • January 22-28
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku Misonkhano—2024
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku Misonkhano—2024
mwb24 January masa. 6-7

JANUARY 22-28

YOBU 38-39

Nyimbo 11 na Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Kodi Mumapatula Nthawi Kuyang’ana Zacilengedwe?

(Mph. 10)

Atalenga dziko lapansi, Yehova anapatula nthawi yoyang’ana zinthu zimene analenga (Gen. 1:​10, 12; Yobu 38:​5, 6; w21.08 9 ¶7)

Angelo nawonso anapatula nthawi yoyang’ana cilengedwe ca Yehova (Yobu 38:7; w20.08 14 ¶2)

Timalimbikitsa cikhulupililo cathu mwa Yehova tikamapatula nthawi yoyang’ana zacilengedwe na kuziyamikila (Yobu 38:​32-35; w23.03 17 ¶8)

Mayi na mwana wake wamng’ono ali panja ndipo akusangalala pomwe akuona gulugufe.

2. Kufufuza Cuma Cauzimu

(Mph. 10)

  • Yobu 38:​8-10—Kodi mavesiwa aonetsa bwanji kuti Yehova ndiye woyenela kupeleka malamulo? (it-2 222)

  • Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zomwe mungakonde kutigaŵilako?

3. Kuŵelenga Baibo

(Mph. 4) Yobu 39:​1-22 (th phunzilo 5)

CITANI KHAMA PA ULALIKI

4. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 2) ULALIKI WAMWAYI. Thetsani makambilanowo mwaulemu mukaona kuti munthuyo safuna kukambilana. (lmd phunzilo 2 mfundo 3)

5. Kubwelelako

(Mph. 5) NYUMBA NA NYUMBA. Pa ulendo wapita, munthuyo anakuuzani kuti posacedwa anataikilidwa wokondedwa wake mu imfa. (lmd phunzilo 9 mfundo 3)

6. Nkhani

(Mph. 5) lmd zakumapeto A mfundo 1—Mutu: Zocitika pa Dziko na Makhalidwe a Anthu Zionetsa Kuti Posacedwa Zinthu Zidzasintha. (th phunzilo 16)

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Nyimbo 111

7. Kuyang’ana Zacilengedwe Kumatithandiza Kukhala na Maganizo Oyenela

(Mph. 15) Kukambilana.

Yobu akuganizila zokhudza zina mwa zinthu zocititsa cidwi zomwe Yehova analenga, kuphatikizapo mvuwu, dokowe, nthiwatiwa, ng’ona, ciwombankhanga, hosi, na njati. Mphepo yamphamvu ikuwomba ndipo Elihu limodzi ni anzake atatu acinyengo a Yobu, akhala naye capafupi.

Pamene Yobu anali kuvutitsidwa na Satana komanso anzake atatu, iye anali kuganizila kwambili mavuto ake na kunenezedwa kwake kopanda cilungamo.

Ŵelengani Yobu 37:14. Kenako funsani omvela kuti:

Kodi Yobu anafunika kucita ciyani kuti akhalenso wolimba mwauzimu?

Tikalefulidwa na mayeso amene tingakumane nawo, kuyang’ana zacilengedwe kungatithandize kukumbukila ukulu wa Yehova, kulimbikitsa cikhumbo cathu cokhalabe wokhulipilika kwa iye, komanso kukulitsa cidalilo cathu cakuti iye ali na mphamvu zokwanitsa kutithandiza.—Mat. 6:26.

Tambitsani VIDIYO yakuti Zimene Tiphunzila pa Nkhani Yokhala Wokhulupilika m’Buku la Yobu—Pa Nyama Zimene Mulungu Analenga. Kenako funsani omvela kuti:

Kodi vidiyo iyi yalimbikitsa bwanji cikhulupililo canu mwa Yehova?

8. Phunzilo la Baibo la Mpingo

(Mph. 30) bt mutu 4 ¶13-20

Mawu Othela (Mph. 3) | Nyimbo 54 na Pemphelo

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani