LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb24 March masa. 9-16
  • April 1-7

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • April 1-7
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku Misonkhano—2024
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku Misonkhano—2024
mwb24 March masa. 9-16

APRIL 1-7

MASALIMO 23-25

Nyimbo 4 na Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. “Yehova ni M’busa Wanga”

(Mph. 10)

Yehova amatitsogolela (Sal. 23:1-3; w11 5/1 31 ¶3)

Yehova amatiteteza (Sal. 23:4; w11 5/1 31 ¶4)

Yehova amatidyetsa (Sal. 23:5; w11 5/1 31 ¶5)

M’busa mwanyamula mwana wa nkhosa ndipo akumutonthoza.

Yehova amasamalila atumiki ake mmene m’busa wacikondi amasamalila nkhosa zake.

DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi Yehova wakhala akunisamalila motani?’

2. Kufufuza Cuma Cauzimu

(Mph. 10)

  • Sal. 23:3—Kodi ‘njila zacilungamo’ n’ciyani? Nanga tingacite ciyani kuti tisapatukemo? (w11 2/15 24 ¶1-3)

  • Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutigaŵilako?

3. Kuŵelenga Baibo

(Mph. 4) Sal. 23:1–24:10 (th phunzilo 5)

CITANI KHAMA PA ULALIKI

4. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 3) ULALIKI WAMWAYI. Ŵelengani vesi yolimbikitsa munthu amene wakuuzani kuti ali na nkhawa cifukwa ca zacilengedwe zimene zawonongeka. (lmd phunzilo 2 mfundo 5)

5. Kubwelelako

(Mph. 4) KUNYUMBA NA NYUMBA. Onetsani munthu amene munam’gaŵila bulosha yakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! mmene phunzilo la Baibo limacitikila. (lmd phunzilo 9 mfundo 3)

6. Kupanga Ophunzila

(Mph. 5) lff phunzilo 14 mfundo 4 (lmd phunzilo 11 mfundo 3)

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Nyimbo 54

7. Timakana Mawu a Alendo

( (Mph. 15) Kukambilana.

M’busa na mlendo onse akuitana nkhosa zimodzimodzi. Nkhosa zikumvela m’busa wawo na kumutsatila.

Nkhosa zimadziŵa mawu a m’busa wawo ndipo zimamutsatila. Koma zimathaŵa mlendo amene sizidziŵa mawu ake. (Yoh. 10:5) Mofananamo, timamvela mawu a Yehova na Yesu omwe ni Abusa athu auzimu, acikondi komanso odalilika. (Sal. 23:1; Yoh. 10:11) Koma timakana mawu a alendo amene amafuna kufooketsa cikhulupililo cathu pokamba “mawu acinyengo.”—2 Pet. 2:1, 3.

Genesis caputala 3 imakamba za nthawi pamene mawu a mlendo anamveka koyamba pa dziko lapansi. Satana anasoceletsa Hava mwa kulankhula naye poseŵenzetsa njoka. Iye ananamizila kukhala bwenzi la Hava, ndipo anapotoza mawu a Yehova komanso zolinga zake. N’zacisoni kuti Hava anamumvela, ndipo zinabweletsa mavuto aakulu pa iye na banja lake.

Masiku ano, Satana amatipangitsa kuyamba kukayikila gulu la Yehova, pofalitsa nkhani zosoceletsa komanso mabodza amkunkhuniza. Tikamva mawu a alendo tiyenela kuthaŵa! Kumvetsela mawuwo ngakhale kwa nthawi yocepa pofuna kudziŵa zina zake n’koopsa. Kodi Satana anaseŵenzetsa mawu angati posoceletsa Hava pa makambilano awo acidule? (Gen. 3:1, 4, 5) Koma bwanji ngati munthu amene timam’dziŵa ndipo amatikonda na kutifunila zabwino, afuna kutiuza zinthu zoipa zokhudza gulu la Yehova?

Tambitsani VIDIYO yakuti Kanani “Mawu a Alendo.” Kenako funsani omvela kuti:

Kodi mwaphunzila ciyani kwa Rose mmene anacitila zinthu na amayi ake amene si mboni?

8. Phunzilo la Baibo la Mpingo

(Mph. 30) bt mutu 8 ¶1-4, mabokosi pa mas. 61-62

Mawu Othela (Mph. 3) | Nyimbo 55 na Pemphelo

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani