LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb24 May masa. 14-16
  • June 24-30

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • June 24-30
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku Misonkhano—2024
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku Misonkhano—2024
mwb24 May masa. 14-16

JUNE 24-30

MASALIMO 54-56

Nyimbo 48 na Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Mulungu Ali Kumbali Yanu

(Mph. 10)

Mofanana na Davide, dalilani Yehova mukacita mantha (Sal. 56:​1-4; w06-CN 8/1 22 ¶10-11)

Yehova amayamikila kupilila kwanu ndipo adzakuthandizani (Sal. 56:8; cl-CN 243 ¶9)

Yehova ali kumbali yanu. Iye sadzalola kuti cinthu ciliconse cikuvulazeni kwamuyaya (Sal. 56:​9-13; Aroma 8:​36-39; w22.06 18 ¶16-17)

Mlongo wovutika maganizo akupemphela mocokela pansi pa mtima.

2. Kufufuza Cuma Cauzimu

(Mph. 10)

  • Sal. 55:​12, 13—Kodi Yehova anakonzelatu zoti Yudasi akapeleke Yesu? (it-1-E 857-858)

  • Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutigaŵilako?

3. Kuŵelenga Baibo

(Mph. 4) Sal. 55:​1-23 (th phunzilo 10)

CITANI KHAMA PA ULALIKI

4. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 3) ULALIKI WAPOYELA. Uzani munthu za pulogilamu yathu yophunzitsa Baibo, ndipo m’patseni kakhadi kopemphela phunzilo la Baibo. (th phunzilo 11)

5. Kubwelelako

(Mph. 4) ULALIKI WAMWAYI. (lmd phunzilo 7 mfundo 4)

6. Nkhani

(Mph. 5) w23.01 29-30 ¶12-14—Mutu: Cikondi Cathu pa Khristu Cimatilimbikitsa Kukhala Olimba Mtima. Onani cithunzi. (th phunzilo 9)

Mlongo ali mu basi ndipo akuyang’ana mtsikana amene akuoneka wovutika maganizo. Mlongoyo wanyamula kathilakiti kakuti “Tingapeze Kuti Mayankho a Mafunso Ofunika Kwambili Onena za Umoyo?”

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Nyimbo 153

7. Tingakhalebe Okondwela Ngakhale . . . Pa Lupanga

(Mph. 5) Kukambilana.

Cithunzi ca m’vidiyo yakuti “Tingakhalebe Okondwela Ngakhale . . . Pa Lupanga.” M’bale Dugbe akuganizila zimene zinamucitikila.

Tambitsani VIDIYO. Kenako funsani omvela kuti:

  • Kodi pa zimene zinacitikila m’bale Dugbe mwaphunzilapo ciyani cokuthandizani mukacita mantha?

8. Vidiyo yakuti Zimene Gulu Lakwanitsa Kucita ya June

(Mph. 10) Tambitsani VIDIYO.

9. Phunzilo la Baibo la Mpingo

(Mph. 30) bt mutu 11 ¶11-19

Mawu Othela (Mph. 3) | Nyimbo 70 na Pemphelo

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani