JUNE 17-23
MASALIMO 51-53
Nyimbo 89 na Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)
1. Zimene Mungacite Kuti Mupewe Macimo Akulu-akulu
(Mph. 10)
Musamadzidalile cifukwa munthu aliyense akhoza kucita zoipa (Sal. 51:5; 2 Akor. 11:3)
Khalani na pulogilamu yabwino yocita zinthu zauzimu nthawi zonse (Sal. 51:6; w19.01 15 ¶4-5)
Pewani maganizo oipa na zilakolako zonyansa (Sal. 51:10-12; w15 6/15 14 ¶5-6)
2. Kufufuza Cuma Cauzimu
(Mph. 10)
Sal. 52:2-4—Kodi mavesiwa akutiuza kuti Doegi anali munthu wotani? (it-1-E 644)
Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutigaŵilako?
3. Kuŵelenga Baibo
(Mph. 4) Sal. 51:1-19 (th phunzilo 12)
4. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 2) ULALIKI WAPOYELA. (lmd phunzilo 7 mfundo 3)
5. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 2) KU NYUMBA NA NYUMBA. (lmd phunzilo 4 mfundo 4)
6. Kubwelelako
(Mph. 3) ULALIKI WAMWAYI. Phunzitsani munthuyo dzina la Mulungu. (lmd phunzilo 9 mfundo 5)
7. Kupanga Ophunzila
Nyimbo 115
8. Zimene Mungacite Kuti Mukonze Zolakwa Zanu
(Mph. 15) Kukambilana.
Ngakhale timayesetsa kucita zinthu zoyenela, tonse timalakwitsabe. (1 Yoh. 1:8) Tikalakwa tisalole manyazi kapena mantha oopa cilango kutilepheletsa kupempha Yehova kuti atikhululukile na kutithandiza. (1 Yoh. 1:9) Kupemphela kwa Yehova ndico cinthu coyamba cimene cingatithandize kukonza zolakwa zathu.
Ŵelengani Salimo 51:1, 2, 17. Kenako funsani omvela kuti:
Kodi mawu a Davide amatilimbikitsa bwanji kupemphela kwa Yehova tikacita chimo lalikulu?
Tambitsani VIDIYO YAKUTI Umoyo Wanga Nili Wacinyamata—Kodi Ningakonze Bwanji Zolakwa Zanga? Kenako funsani omvela kuti:
Kodi ni zinthu zotani zinapangitsa kuti Thalila na José alakwitse zinthu?
Kodi anacita ciyani kuti akonze zolakwa zawo?
Kodi kucita zimenezi kunawapindulila bwanji?
9. Phunzilo la Baibo la Mpingo
(Mph. 30) bt mutu 11 ¶5-10, bokosi pa tsa. 89