LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb24 July masa. 6-7
  • July 22-28

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • July 22-28
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku Misonkhano—2024
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku Misonkhano—2024
mwb24 July masa. 6-7

JULY 22-28

MASALIMO 66-68

Nyimbo 7 na Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Yehova Amanyamula Katundu Wathu Tsiku na Tsiku

(Mph. 10)

Yehova amamvela mapemphelo athu na kuwayankha (Sal. 66:19; w23.05 12 ¶15)

Yehova amadziŵa zosoŵa za anthu ovutika (Sal. 68:5; w10-CN 12/1 23 ¶6; w09-CN 4/1 31 ¶1)

Iye amatithandiza tsiku lililonse (Sal. 68:19; w23.01 19 ¶17)

Zithunzi: Mlongo akupemphela pa nthawi zosiyana-siyana. 1. Akupemphela pambuyo pouka. 2. Akupemphela na ana ake asanapite ku sukulu. 3. Akupemphela ku nchito.

ZOFUNIKA KUZISINKHASINKHA: Kodi timamulola bwanji Yehova kunyamula katundu wathu?

2. Kufufuza Cuma Cauzimu

(Mph. 10)

  • Sal. 68:18—Mu Isiraeli wakale, kodi ndani anali “mphatso za amuna”? (w06-CN 6/1 10 ¶5)

  • Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?

3. Kuŵelenga Baibo

(Mph. 4) Sal. 66:​1-20 (th phunzilo 11)

CITANI KHAMA PA ULALIKI

4. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 3) KUNYUMBA NA NYUMBA. Mwini nyumba ni wacikhalidwe cosiyana na canu. (lmd phunzilo 5 mfundo 3)

5. Kubwelelako

(Mph. 4) KUNYUMBA NA NYUMBA. Pitilizani kukambilana kathilakiti kamene munamusiyila ulendo wapita. (lmd phunzilo 9 mfundo 3)

6. Kupanga Ophunzila

(Mph. 5) lff phunzilo 15 mawu oyamba, komanso mfundo 1-3 (th phunzilo 8)

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Nyimbo 102

7. Kodi Mungam’peputsileko Katundu Mkhristu Mnzanu?

(Mph. 15) Kukambilana.

Palibe mtumiki wa Mulungu yemwe amakhala yekha akamalimbana na mavuto. (2 Mbiri 20:15; Sal. 127:1) Yehova ni Mthandizi wathu. (Yes. 41:10) Kodi Yehova amatithandiza m’njila ziti? Amatipatsa malangizo poseŵenzetsa mawu ake na gulu lake. (Yes. 48:17) Amatipatsanso mzimu wake woyela wamphamvu. (Luka 11:13) Amagwilitsa nchito abale na alongo athu kuti atilimbikitse na kutithandiza. (2 Akor. 7:6) Izi zionetsa kuti Yehova angagwilitse nchito aliyense wa ife kupeputsako katundu wa Mkhristu mnzake.

Cithunzi ca mu vidiyo yakuti “Onetsani Cikondi Cosatha mu Mpingo​—Kwa Okalamba.” Mlongo Paulina Sántiz Gómez waimilila panja pa nyumba yake ndipo akumwetulila.

Tambitsani VIDIYO yakuti Onetsani Cikondi Cosatha mu Mpingo—Kwa Okalamba. Kenako funsani omvela kuti:

  • Kodi mungacite ciyani kuti mum’peputsileko katundu Mkhristu wokalamba?

Cithunzi ca mu vidiyo yakuti “Onetsani Cikondi Cosatha mu Mpingo​—Kwa Atumiki Anthawi Zonse.” Joseph DeVito na mkazi wake Anita akuseŵenzela pamodzi mu ulaliki.

Tambitsani VIDIYO yakuti Onetsani Cikondi Cosatha mu Mpingo—Kwa Atumiki Anthawi Zonse. Kenako funsani omvela kuti:

  • Kodi mungacite ciyani kuti mum’peputsileko katundu mtumiki wanthawi zonse?

Cithunzi ca mu vidiyo yakuti “Onetsani Cikondi Cosatha mu Mpingo​—Kwa Alendo Ocokela ku Maiko Ena.” Bill Zeng na mkazi wake Maggie akumwetulila pamene akuphunzila Baibo.

Tambitsani VIDIYO yakuti Onetsani Cikondi Cosatha mu Mpingo—Kwa Alendo Ocokela ku Maiko Ena. Kenako funsani omvela kuti:

  • Kodi mungacite ciyani kuti muŵapeputsileko katundu anthu amene akukumana na mayeso ovuta?

8. Phunzilo la Baibo la Mpingo

(Mph. 30) bt mutu 13 ¶1-7, mawu oyamba a cigawo 5, komanso bokosi pa tsa. 103

Mawu Othela (Mph. 3) | Nyimbo 88 na Pemphelo

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani