LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb24 July masa. 4-5
  • July 15-21

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • July 15-21
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku Misonkhano—2024
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku Misonkhano—2024
mwb24 July masa. 4-5

JULY 15-21

MASALIMO 63-65

Nyimbo 108 na Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. “Cikondi Canu Cokhulupilika Nʼcabwino Kuposa Moyo”

(Mph. 10)

Kukhala pa ubale wabwino na Mulungu n’kofunika kwambili kuposa moyo (Sal. 63:3; w01-CN 10/15 15-16 ¶17-18)

Kuganizila kwambili mmene Yehova wationetsela cikondi cake cokhulupilika kapena kuti cosasintha kudzatithandiza kumuyamikila kwambili (Sal. 63:6; w19.12 28 ¶4; w15 10/15 22 ¶7)

Kuyamikila cikondi cosasintha ca Mulungu kumatilimbikitsa kumutamanda mokondwela (Sal. 63:​4, 5; w09-CN 7/15 16 ¶6)

Zithunzi: Mlongo akuŵelenga Baibo. 1. Akusangalala pamene akuseŵenza na mlongo wina mu ulaliki. 2. Akupeleka ndemanga pa msonkhano.

ZIMENE MUNGACITE PA KULAMBILA KWA PABANJA: Kambilanani mmene Yehova wakuonetselani cikondi cosasintha.

2. Kufufuza Cuma Cauzimu

(Mph. 10)

  • Sal. 64:3—Kodi vesiyi itilimbikitsa bwanji kuti tizilankhula mawu olimbikitsa nthawi zonse? (w07-CN 11/15 15 ¶6)

  • Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?

3. Kuŵelenga Baibo

(Mph. 4) Sal. 63:1–64:10 (th phunzilo 12)

CITANI KHAMA PA ULALIKI

4. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 2) KUNYUMBA NA NYUMBA. Mwini nyumba salankhula cinenelo canu. (lmd phunzilo 3 mfundo 4)

5. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 2) ULALIKI WAMWAYI. Makambilano atha musanamulalikile n’komwe. (lmd phunzilo 2 mfundo 4)

6. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 3) ULALIKI WAPOYELA. Dziŵani nkhani imene ingamucititse cidwi munthuyo, ndipo panganani kuti mukakambilanenso naye pa nthawi ina. (lmd phunzilo 1 mfundo 5)

7. Kufotokoza Zimene Mumakhulupilila

(Mph. 4) Citsanzo. ijwfq 51—Mutu: N’cifukwa Ciyani a Mboni za Yehova Amalalikila Anthu Omwe Anaŵauzapo Kale Kuti Safuna Kuŵalalikila? (lmd phunzilo 4 mfundo 3)

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Nyimbo 154

8. Mmene Timaonetsela Kuti Timakonda Mulungu

(Mph. 15) Kukambilana.

Yehova ni “wacikondi cokhulupilika coculuka.” (Sal. 86:15) Mawu akuti “cikondi cokhulupilika” kapena kuti cikondi cosasintha, amatanthauza cikondi cimene cimaonetsedwa cifukwa ca kudzipeleka, kukhulupilika, kusasunthika, komanso kugwilizana kwambili. Ngakhale kuti Yehova amakonda anthu onse, iye amaonetsa cikondi cimeneci kwa atumiki ake okha, anthu amene ali naye pa ubale wolimba. (Sal. 33:18; 63:3; Yoh. 3:16; Mac. 14:17) Tingasonyeze kuti timayamikila cikondi cosasintha ca Yehova mwa kuonetsa kuti nafenso timamukonda. Motani? Mwa kumvela malamulo ake, kuphatikizapo lamulo la ‘kupanga ophunzila.’—Mat. 28:19; 1 Yoh. 5:3.

Tambitsani VIDIYO yakuti Onetsani Cikondi Cosatha mu Ulaliki. Kenako funsani omvela kuti:

Kodi cikondi cingatilimbikitse bwanji kulalikila uthenga wabwino

    Cithunzi ca mu vidiyo yakuti “Onetsani Cikondi Cosatha mu Ulaliki.” Tate wa mu vidiyo wagona pa mpando pambuyo pokomboka ku nchito.
  • tikakhala olema?

  • Cithunzi ca mu vidiyo yakuti “Onetsani Cikondi Cosatha mu Ulaliki.” Mwininyumba wokwiya akulankhula mwaukali kwa tate amene ali na mwana wake mu utumiki.
  • tikamatsutsidwa?

  • Cithunzi ca mu vidiyo yakuti “Onetsani Cikondi Cosatha mu Ulaliki.” Mayi wa mu vidiyo na mwana wake akukambilana na wogulitsa mu shopu.
  • tikamagwila nchito za tsiku na tsiku?

9. Phunzilo la Baibo la Mpingo

(Mph. 30) bt mutu 12 ¶14-20

Mawu Othela (Mph. 3) | Nyimbo 79 na Pemphelo

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani