LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb24 November masa. 2-16
  • November 4-10

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • November 4-10
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku Misonkhano—2024
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku Misonkhano—2024
mwb24 November masa. 2-16

NOVEMBER 4-10

SALIMO 105

Nyimbo 3 na Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Dziko Lolonjezedwa. Zithunzi: 1. Abulahamu. 2. Isaki. 3. Yakobo.

1. “Amakumbukila Pangano Lake Mpaka Kalekale”

(Mph. 10)

Yehova anacita pangano lake na Abulahamu, ndipo analibwelezanso kwa Isaki komanso Yakobo (Gen. 15:18; 26:3; 28:13; Sal. 105:​8-11)

Kukwanilitsidwa kwa lonjezo limeneli kunaoneka ngati kosatheka (Sal. 105:​12, 13; w23.04 28 ¶11-12)

Yehova sanaiŵale lonjezo lake kwa Abulahamu (Sal. 105:​42-44; it-2-E 1201 ¶2)


DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi kudalilika kwa Yehova kumanilimbikitsa bwanji?’

2. Kufufuza Cuma Cauzimu

(Mph. 10)

  • Sal. 105:​17-19—Kodi “mawu a Yehova” anamuyenga motani Yosefe? (w86-CN 11/1 19 ¶15)

  • Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?

3. Kuŵelenga Baibo

(Mph. 4) Sal. 105:​24-45 (th phunzilo 5)

CITANI KHAMA PA ULALIKI

4. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 1) KUNYUMBA NA NYUMBA. Mwininyumba ni wotangwanika. (lmd phunzilo 2 mfundo 5)

5. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 2) KUNYUMBA NA NYUMBA. Thetsani makambilano anu mwaubwenzi pamene mwininyumba wayambitsa mkangano (lmd phunzilo 4 mfundo 5)

6. Kubwelelako

(Mph. 4) KUNYUMBA NA NYUMBA. Gaŵilani magazini yokhala na nkhani imene mwininyumba anacita nayo cidwi pa ulendo wapita. (lmd phunzilo 8 mfundo 3)

7. Kubwelelako

(Mph. 4) ULALIKI WAMWAYI. Muuzeni za JW Laibulale® ndipo muthandizeni kuicita daunilodi. (lmd phunzilo 9 mfundo 5)

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Nyimbo 84

8. Mmene Mungaonetsele Kuti Mumam’konda Yesu

(Mph. 15) Kukambilana.

Tikamaseŵenzetsa nthawi yathu, mphamvu zathu, komanso cuma cathu popititsa patsogolo nchito ya Ufumu, timaonetsa kuti timaikonda Mfumu yathu Khristu Yesu. Kucita zimenezi kumakondweletsa Yehova komanso abale na alongo athu. (Yoh. 14:23) Nkhani za pa jw.org zakuti “Mmene Zopeleka Zanu Zimagwilila Nchito” zimaonetsa mmene zopeleka zathu zimathandizila kwambili abale na alongo padziko lonse.

Dzanja la munthu amene akuika ndalama m’kabokosi ka zopeleka. Zithunzi: 1. M’bale waima pa maso pa woweluza. 2. Mlongo akugwila nchito zamamangidwe za gulu lathu. 3. Mlongo akutamba vidiyo ya cinenelo ca manja.

Tambitsani VIDIYO yakuti Zopeleka Zanu Zimagwila Nchito Yaikulu. Kenako funsani omvela kuti:

  • Nthawi zina zopeleka zimagwilitsidwa nchito pomenyela ufulu wathu wa kulambila. Kodi izi zawathandiza bwanji abale athu?

  • Kodi kuonetsetsa kuti pali “kufanana” pa kagwilitsidwe nchito ka zopeleka kwathandiza bwanji pomanga Nyumba za Ufumu?—2 Akor. 8:14

  • Kodi pakhala mapindu otani cifukwa coseŵenzetsa zopeleka pomasulila Baibo m’zinenelo zambili?

Dziŵani Zambili pa Intaneti

Kacizindikilo ka “Zopeleka“ koonetsa dzanja limene lagwila kakhobili.

Kodi mungatani kuti mucite copeleka ca ufulu pothandiza pa nchito ya Mboni za Yehova? Mukapita pansi pa tsamba loyamba la JW Laibulale, dinizani pa kacithunzi kolemba kuti “Donations.” M’maiko ambili, mukadiniza pa kacithunzika mudzapeza polemba kuti MOK. Batani imeneyo idzakupelekani ku dokyumenti yolemba kuti Donations to Jehovah’s Witnesses—Frequently Asked Questions.

9. Phunzilo la Baibo la Mpingo

(Mph. 30) bt mutu 17 ¶13-19

Mawu Othela (Mph. 3) | Nyimbo 97 na Pemphelo

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani