LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb24 November masa. 6-7
  • November 25–December 1

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • November 25–December 1
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku Misonkhano—2024
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku Misonkhano—2024
mwb24 November masa. 6-7

NOVEMBER 25–DECEMBER 1

MASALIMO 109-112

Nyimbo 14 na Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Thandizilani Yesu Amene ni Mfumu!

(Mph. 10)

Yesu atabwelela kumwamba, anakhala ku dzanja lamanja la Yehova (Sal. 110:1; w06-CN 9/1 13 ¶6)

Mu 1914, Yesu anayamba kugonjetsa adani ake (Sal. 110:2; w00-CN 4/1 18 ¶3)

Tiyenela kudzipeleka na mtima wonse pothandizila ulamulilo wa Yesu (Sal. 110:3; be 76 ¶2)

Zithunzi: M’bale wacinyamata akucilikiza ulamulilo wa Yesu. 1. Akuthandizila kupeleka mamaikolofoni pa msonkhano wa mpingo. 2. Akuthandiza mlongo wacikulile amene ali pa njinga ya olumala. 3. Akucita phunzilo la Baibo la munthu mwini. 4. Akuphunzitsidwa na m’bale wina mmene angasamalilile utumiki winawake pa mpingo.

DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi n’zolinga ziti zimene ningadziikile zoonetsa kuti nikuthandiza pa nchito ya Ufumu?’

2. Kufufuza Cuma Cauzimu

(Mph. 10)

  • Sal. 110:4—Fotokozani pangano lochulidwa pa vesili. (it-1-E 524 ¶2)

  • Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?

3. Kuŵelenga Baibo

(Mph. 4) Sal. 109:​1-26 (th phunzilo 2)

CITANI KHAMA PA ULALIKI

4. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 2) KUNYUMBA NA NYUMBA. Seŵenzetsani thilakiti poyambitsa makambilano. (lmd phunzilo 4 mfundo 3)

5. Kufotokoza Zimene Mumakhulupilila

(Mph. 5) Citsanzo. ijwfq 23—Mutu: N’chifukwa Chiyani Simupita Kunkhondo? (lmd phunzilo 4 mfundo 4)

6. Kupanga Ophunzila

(Mph. 5) lff phunzilo 15 mfundo 6 komanso mbali yakuti Anthu Ena Amakamba Kuti (lmd phunzilo 11 mfundo 3)

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Nyimbo 72

7. Tingacite Ciyani Pocilikiza Ufumu Mokhulupilika?

(Mph. 15) Kukambilana.

Cithunzi ca m’vidiyo yakuti “Thandizilani ‘Kalonga Wamtendele’ Mokhulupilika.” Abale aŵili akulalikila mwamuna pa gombe.

Ufumu wa Yehova ni njila imene iye amaonetsela mphamvu zake monga Wolamulila wa cilengedwe conse. (Dan. 2:​44, 45) Conco, tikamayesetsa kucita zinthu zoonetsa kuti tili ku mbali ya Ufumu wa Mulungu, timasonyeza kuti timakhulupilila kuti Yehova ndiye wolamulila wabwino koposa.

Tambitsani VIDIYO Yakuti Thandizilani “Kalonga Wamtendele” Mokhulupilika. Ndiyeno funsani omvela kuti:

  • Kodi ni motani mmene timathandizila Ufumu wa Mulungu mokhulupilika?

Lembani lemba logwilizana na mfundo iliyonse pansipa poonetsa mmene tingakhalile ku mbali ya Ufumu wa Mulungu.

  • Kuika Ufumu wa Mulungu patsogolo mu umoyo wathu.

  • Kutsatila mfundo za makhalidwe abwino zimene nzika za Ufumu ziyenela kutsatila.

  • Kulalikila mwakhama uthenga wa Ufumu.

  • Kuonetsa ulemu kwa olamulila a boma, kwinaku tikumvela Mulungu ngati malamulo a Kaisara akutsutsana na malamulo a Mulungu.

8. Phunzilo la Baibo la Mpingo

(Mph. 30) bt mutu 18 ¶16-24

Mawu Othela (Mph. 3) | Nyimbo 75 na Pemphelo

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani