LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb24 November masa. 14-16
  • December 30, 2024–January 5, 2025

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • December 30, 2024–January 5, 2025
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku Misonkhano—2024
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku Misonkhano—2024
mwb24 November masa. 14-16

DECEMBER 30, 2024–JANUARY 5, 2025

MASALIMO 120-126

Nyimbo 144 na Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Aisiraeli akukolola tiligu woculuka mwacisangalalo.

Aisiraeli amene anabwelela kwawo akukolola mbewu mwacisangalalo cifukwa Yehova wadalitsa khama lawo

1. Anabyala Akulila, koma Anakolola Akusangalala

(Mph. 10)

Aisiraeli anasangalala atamasulidwa ku ukapolo ku Babulo kuti akabwezeletse kulambila koona (Sal. 126:​1-3)

Aisiraeli amene anabwelela ku Yudeya analila, mwina cifukwa ca kukula kwa nchito imene anafunika kugwila (Sal. 126:5; w04-CN 6/1 16 ¶10)

Koma iwo analimbikila kugwila nchitoyo ndipo anadalitsidwa (Sal. 126:6; w21.11 24 ¶17; w01-CN 7/15 18-19 ¶13-14; onani cithunzi )

Aisiraeli akugwila nchito mwakhama polima nthaka. Mwamuna m’modzi akubyala mbewu pamene wina akugaula.

ZOFUNIKA KUZISINKHASINKHA: Pambuyo populumutsidwa pa nkhondo ya Aramagedo, kodi n’zovuta ziti zimene tidzakumana nazo pokonzanso dzikoli? Nanga tidzapeza madalitso otani?

2. Kufufuza Cuma Cauzimu

(Mph. 10)

  • Sal. 124:​2-5—Kodi tiyenela kuyembekezela kuti Yehova adzateteza moyo wathu ngati mmene anacitila kwa Aisiraeli? (cl-CN 73 ¶15)

  • Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?

3. Kuŵelenga Baibo

(Mph. 4) Sal. 124:1–126:6 (th phunzilo 5)

CITANI KHAMA PA ULALIKI

4. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 3) ULALIKI WAPOYELA. (lmd phunzilo 3 mfundo 5)

5. Kubwelelako

(Mph. 4) KUNYUMBA NA NYUMBA. Pa makambilano apita, munthuyo anaonetsa kuti sakhulupilila Baibo. (lmd phunzilo 9 mfundo 5)

6. Kupanga Ophunzila

(Mph. 5) lff phunzilo 16 mawu oyamba komanso mfundo 1-3 (lmd phunzilo 11 mfundo 3)

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Nyimbo 155

7. Kondwelani na Malonjezo a Mulungu

(Mph. 15.) Kukambilana.

Yehova anakwanilitsa zimene analonjeza kwa anthu amene anagwidwa ukapolo ku Babulo. Anawapulumutsa na kuwacilitsa mwauzimu. (Yes. 33:24) Iye anateteza anthuwo komanso ziweto zawo ku mikango yolusa komanso zilombo zina zimene zinali zitaculuka pa nthawiyo. (Yes. 65:25) Iwo anali kukhala m’nyumba zawo-zawo komanso kudya zipatso za m’minda yawo ya mpesa. (Yes. 65:21) Mulungu anadalitsa nchito yawo, ndipo iwo anakhala na moyo wautali.—Yes. 65:​22, 23.

Zithunzi za mu vidiyo yakuti “Kondwelani na Malonjezo a Mulungu Okamba za Mtendele​—Mbali Yake. Zithunzi: 1. Abale na alongo akusangalala na maceza. 2. Mapili na nkhalango. 3. Mneneli Danieli amene waukitsidwa kwa akufa akuyenda mu nkhalango. 4. Makolo akukumbatila mtsikana wawo amene waukitsidwa. 5. Zipatso na zakudya zamasamba. 6. Mathithi a madzi.

Waterfall: Maridav/stock.adobe.com; mountains: AndreyArmyagov/stock.adobe.com

Tambitsani VIDIYO Yakuti Kondwelani na Malonjezo a Mulungu Okamba za Mtendele—Mbali Yake. Ndiyeno funsani omvela kuti:

  • Kodi maulosi amenewa akukwanilitsika motani masiku ano?

  • Nanga adzakwanilitsika motani pa mlingo waukulu m’dziko latsopano?

  • Kodi ni ulosi uti umene inu mukuuyembekezela mwacidwi?

8. Phunzilo la Baibo la Mpingo

(Mph. 30) bt mutu 20 ¶8-12, bokosi pa tsa. 161

Mawu Othela (Mph. 3) | Nyimbo 58 na Pemphelo

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani