LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb24 November masa. 12-13
  • December 23-29

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • December 23-29
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku Misonkhano—2024
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku Misonkhano—2024
mwb24 November masa. 12-13

DECEMBER 23-29

SALIMO 119:​121-176

Nyimbo 31 na Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Mmene Tingapewele Kudzibweletsela Zopweteka

(Mph. 10)

Muzikonda malamulo a Mulungu (Sal. 119:127; w18.06 17 ¶5-6)

Muzidana na zoipa (Sal. 119:128; w93-CN 4/15 17 ¶12)

Mvelani Yehova kuti mupewe kulakwitsa zinthu ngati mmene anthu ‘osadziŵa zambili’ amacitila (Sal. 119:​130, 133; Miy. 22:3)

Baibo yotseguka pafupi na makoini komanso mitanda ya golide.

DZIFUNSENI KUTI, ‘N’zinthu ziti zimene niyenela kuwongolela poonetsa kuti nimakonda kwambili malamulo a Mulungu kapena kudana na zoipa?’

2. Kufufuza Cuma Cauzimu

(Mph. 10)

  • Sal. 119:160—Malinga na vesili, kodi tiyenela kukhala otsimikiza za ciyani? (w23.01 2 ¶2)

  • Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?

3. Kuŵelenga Baibo

(Mph. 4) Sal. 119:​121-152 (th phunzilo 2)

CITANI KHAMA PA ULALIKI

4. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 3) KUNYUMBA NA NYUMBA (lmd phunzilo 1 mfundo 5)

5. Kubwelelako

(Mph. 4) KUNYUMBA NA NYUMBA Muonetseni mopezela nkhani imene ingamucititse cidwi pa jw.org. (lmd phunzilo 8 mfundo 3)

6. Kupanga Ophunzila

(Mph. 5) Kambilanani na wophunzila Baibo amene sapezeka pa misonkhano ya mpingo kaŵili-kaŵili. (lmd phunzilo 12 mfundo 4)

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Nyimbo 121

7. Musadzibweletsele Zopweteka Cifukwa Cokonda Ndalama

(Mph. 15) Kukambilana.

Anthu amene amakonda ndalama “adzibweletsela zopweteka zambili pathupi lawo.” (1 Tim. 6:​9, 10) Pansipa pandandalikidwa mavuto amene tingakumane nawo ngati timakonda ndalama komanso ngati timaziona kuti ndizo zofunika ngako pa moyo wathu.

  • Sitingakhale paubale wolimba na Yehova. —Mat. 6:24

  • Sitidzakhala wokhutila.—Mlal. 5:10

  • Cingakhale covuta kupewa makhalidwe oipa monga kunama, kuba, komanso cinyengo. (Miy. 28:20) Izi zingapangitse kuti cikumbumtima cathu cizitivutitsa, ndiponso tingawononge mbili yathu komanso ubwenzi wathu na Yehova

Cithunzi ca m’vidiyo yakuti “Mmene Mungaseŵenzetsele Ndalama Zanu.” Kamnyamata kagwila cosungilamo ndalama.

Ŵelengani Aheberi 13:​5, kenako kambilanani funso ili:

  • Kodi ndalama tiyenela kuziona bwanji kuti tipewe zopweteka? Nanga n’cifukwa ciyani?

Ngakhale kuti sitikonda ndalama, tingakumanebe na zopweteka ngati sitizigwilitsa nchito mwanzelu.

Tambitsani vidiyo ya TUKADOLI TOJAMBULA PAMANJA Yakuti Mmene Mungaseŵenzetsele Ndalama Zanu. Kenako funsani omvela mafunso awa:

    Cithunzi ca m’vidiyo yakuti “Mmene Mungaseŵenzetsele Ndalama Zanu.” Mnyamata na mtsikana akulemba zimene afuna kugula komanso mitengo yake. Zimene mnyamata walemba ziphatikizapo mahedifoni, nsapato, cakudya komanso matiketi a sitima. Zimene mtsikana walemba ziphatikizapo cikwama, nkholoko, cakudya komanso mafuta a galimoto.
  • N’cifukwa ciyani tiyenela kupanga bajeti? Nanga tingacite bwanji zimenezi?

  • Cithunzi ca m’vidiyo yakuti “Mmene Mungaseŵenzetsele Ndalama Zanu.” Mtsikana akugula maambulela aŵili mvula ikugwa. Ambulela imodzi ni yake pamene inayo ni ya mlongosi wake amene ndalama yake agulila ayisikilimu
  • N’cifukwa ciyani ni bwino kumasungako ndalama?

  • Cithunzi ca m’vidiyo yakuti “Mmene Mungaseŵenzetsele Ndalama Zanu.” Mnyamata amangidwa ku khadi lalikulu la kubanki pomwe khadi lina la kubanki likusekelela.
  • N’cifukwa ciyani tiyenela kupewa nkhongole zosafunikila?

8. Phunzilo la Baibo la Mpingo

(Mph. 30) bt mutu 20 ¶1-7, komanso mawu oyamba a cigawo 7

Mawu Othela (Mph. 3) | Nyimbo 101 na Pemphelo

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani