LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb25 January masa. 5-16
  • January 20-26

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • January 20-26
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku Misonkhano—2025
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku Misonkhano—2025
mwb25 January masa. 5-16

JANUARY 20-26

MASALIMO 138-139

Nyimbo 93 na Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Musalole Mantha Kukulepheletsani Kutengako Mbali pa Misonkhano

(Mph. 10)

Timafuna kutamanda Yehova na mtima wathu wonse (Sal. 138:1)

Mukacita mantha pamene mukufuna kutengako mbali pa misonkhano, muzidalila Yehova kuti akuthandizeni (Sal. 138:3)

Kucita mantha kungaonetse kuti muli na khalidwe labwino (Sal. 138:6; w19.01 10 ¶10)

Mlongo wakweza dzanja lake kuti apelekepo ndemanga pa msonkhano wa mpingo.

ZOYENELA KUCITA: Mayankho anu azikhala aafupi. Izi zidzakuthandizani kucepetsa mantha.​—w23.04 21 ¶7.

2. Kufufuza Cuma Cauzimu

(Mph. 10)

  • Sal. 139:​21, 22​—Kodi Akhristu ayenela kukhululukila munthu aliyense? (it-1-E 862 ¶4)

  • Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?

3. Kuŵelenga Baibo

(Mph. 4) Sal. 139:​1-18 (th phunzilo 2)

CITANI KHAMA PA ULALIKI

4. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 3) ULALIKI WAPOYELA. (lmd phunzilo 2 mfundo 3)

5. Kupanga Ophunzila

(Mph. 4) ULALIKI WAPOYELA. M’pempheni kuti muziphunzila naye Baibo ndipo muonetseni mmene timacitila. (lmd phunzilo 10 mfundo 3)

6. Nkhani

(Mph. 5) ijwyp nkhani 105​—Mutu: Mungatani Kuti Musamacite Manyazi Kwambili? (th phunzilo 16)

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Nyimbo 59

7. Mungapambane mu Utumiki Wanu Ngakhale Kuti Ndinu Wamanyazi

(Mph. 15) Kukambilana.

Kodi ndinu wamanyazi? Kodi mumafuna kuti ena asakuoneni? Kodi mumacita mantha mukangoganizila zokambilana na anthu ena? Nthawi zina, manyazi angatilepheletse kucita zinthu zimene tingafune kucita. Komabe, ambili amene anali na vuto la manyazi akwanitsa kuuzako ena za Baibo na kupeza cimwemwe pa utumiki wawo. Ndiye tingaphunzile ciyani ku citsanzo cawo?

Tambitsani VIDIYO YAKUTI Nimatumikila na Mtima Wonse Ngakhale Kuti Ndine Wamanyazi. Kenako funsani omvela kuti:

  • Kodi Mlongo Lee anapindula bwanji cifukwa cotsatila malangizo a agogo ake akuti ayenela “kutumikila Yehova na mtima wonse”?

Baibo imaonetsa kuti Mose, Yeremiya na Timoteyo ayenela kuti anali amanyazi. (Eks. 3:11; 4:10; Yer. 1:​6-8; 1 Tim. 4:12) Komabe, iwo anakwanitsa kucita zinthu zazikulu potumikila Yehova cifukwa iye anali nawo. (Eks. 4:12; Yer. 20:11; 2 Tim. 1:​6-8)

Zithunzi: 1. Mose wanyamula miyala iŵili pamene panalembedwa malamulo khumi. 2. Yeremiya akupemphela. 3. Timoteyo akuŵelenga mpukutu.

Ŵelengani Yesaya 43:​1, 2. Kenako funsani omvela kuti:

  • Kodi Yehova anawalonjeza ciyani alambili ake?

Kodi Yehova angawathandize bwanji anthu amanyazi kuti apambane mu utumiki wawo?

Tambitsani VIDIYO YAKUTI Mmene Ubatizo Wanu Ungakubweletseleni Cimwemwe Cacikulu​—Mbali Yake. Ndiyeno funsani omvela kuti:

  • Pa utumiki wake, kodi Mlongo Jackson anaiona motani thandizo Yehova?

  • Kodi utumiki ungamuthandize motani munthu wamanyazi?

8. Phunzilo la Baibo la Mpingo

(Mph. 30) bt mutu 21 ¶8-13, bokosi pa tsa. 169

Mawu Othela (Mph. 3) | Nyimbo 151 na Pemphelo

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani