LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb25 March masa. 2-16
  • March 3-9

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • March 3-9
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku Misonkhano—2025
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku Misonkhano—2025
mwb25 March masa. 2-16

MARCH 3-9

MIYAMBO 3

Nyimbo 8 ndi Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Muzionetsa kuti Mumadalila Yehova

(Mph. 10)

Muzikhulupilila Yehova, m’malo modzidalila (Miy. 3:5; ijwbv nkhani 14 ¶4-5)

Onetsani kuti mumadalila Yehova mwa kufunafuna malangizo ake ndi kuwatsatila (Miy 3:6; ijwbv nkhani 14 ¶6-7)

Pewani kudalila luso lanu lomvetsa zinthu (Miy. 3:7; be-CN 76 ¶4)

Mlongo wacitsikana akugwilitsa nchito tabuleti pofufuza zolinga zam’tsogolo zimene angadziikile. Kumanzele kwake kuli mabulosha okamba za maphunzilo a kudziko. Kulamanja kuli fomu yofunsila kuwonjezela utumiki wake komanso mabuku ofotokoza umoyo wa pa Beteli.

DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi nimafunafuna malangizo a Yehova m’zocita zanga zonse?’

2. Kufufuza Cuma Cauzimu

(Mph. 10)

  • Miy. 3:3​—Kodi tingamange bwanji cikondi cokhulupilika komanso kukhulupilika m’khosi mwathu ndi kuzilemba pamtima pathu? (w06-CN 9/15 17 ¶7)

  • Pa kuwelenga Baibulo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?

3. Kuwelenga Baibulo

(Mph. 4) Miy. 3:​1-18 (th phunzilo 12)

CITANI KHAMA PA ULALIKI

4. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 3) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Onetsani mmene mungayankhile munthu amene wakamba mawu ofala kwanuko ofuna kukanila ulaliki. (lmd phunzilo 1 mfundo 5)

5. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 4) ULALIKI WAPOYELA. Muuzeni za webusaiti ya jw.org ndi kumusiyila kakhadi koloŵela pa webusaiti imeneyi. (lmd phunzilo 3 mfundo 3)

6. Nkhani

(Mph. 5) w11-CN 3/15 14 ¶7-10​—Mutu: Muzidalila Mulungu Mukakumana ndi Anthu Opanda Cidwi mu Ulaliki. (th phunzilo 20)

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Nyimbo 124

7. Muzionetsa kuti Mumadalila Gulu la Yehova

(Mph. 15) Kukambilana.

N’cosavuta kukhulupilila Mawu a Mulungu ouzilidwa a coonadi ca m’Baibulo. Komabe, cimakhala covuta kutsatila malangizo ocokela kwa anthu opanda ungwilo amene amatsogolela gulu la Yehova, makamaka ngati sitinawamvetse malangizowo kapena kugwilizana nawo.

Welengani Malaki 2:7. Kenako funsani omvela kuti:

  • N’cifukwa ciyani n’zosadabwitsa kuti Yehova amagwilitsa nchito anthu opanda ungwilo kutsogolela anthu ake?

Welengani Mateyo 24:45. Kenako funsani omvela kuti:

  • N’cifukwa ciyani tiyenela kuwakhulupilila malangizo ocokela ku gulu la Yehova?

Welengani Aheberi 13:17. Kenako funsani omvela kuti:

  • N’cifukwa ciyani tiyenela kutsatila malangizo ocokela kwa anthu amene Yehova amawagwilitsa nchito kuti atitsogolele?

M’bale wapeleka bokosi la cakudya ku banja linalake. Onse avala mamasiki ndipo akutsanzikana capatali atakweza manja.
Mlongo akupeleka ndemanga pa msonkhano wa mpingo. M’bale wamugwilila maikolofoni pamene akuyankha. Onse pamsonkhanowo avala mamasiki.

Tambitsani kambali ka VIDIYO YAKUTI Ciunikilo Na. 9 ca Bungwe Lolamulila mu 2021. Kenako funsani omvela kuti:

  • Kodi malangizo amene tinalandila pa nthawi ya mlili anakuthandizani bwanji kuti muzilikhulupilila kwambili gulu la Yehova?

8. Phunzilo la Baibulo la Mpingo

(Mph. 30) bt mutu 23 ¶9-15, mabokosi pa mas. 184 ndi 186

Mawu Othela (Mph. 3) | Nyimbo 57 ndi Pemphelo

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani