LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb25 May masa. 2-3
  • May 5-11

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • May 5-11
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku Misonkhano—2025
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku Misonkhano—2025
mwb25 May masa. 2-3

MAY 5-11

MIYAMBO 12

Nyimbo 101 ndi Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Kugwila Nchito Mwakhama Kumapindulitsa

(Mph. 10)

Musamataye nthawi kufunafuna zinthu zopanda pake (Miy. 12:11)

Muzigwila nchito mwakhama (Miy. 12:24; w16.06 30 ¶5)

Mudzafupidwa cifukwa cogwila nchito mwakhama (Miy. 12:14)

Zithunzi: M’bale akugwila nchito mwakhama poika mapaipi komanso pocita zinthu zauzimu. 1. Akuyenda atanyamula zida zake zogwilila nchito. 2. Akugwilitsa nchito sipanala pomanga paipi yaikulu. 3. Ali pa msonkhano wa mpingo limodzi ndi banja lake. Iye ndi mwana wake wamkazi aimika manja kuti apelekepo ndemanga. 4. Akugwilitsa nchito kathilakiti polalikila mwamuna wina pa malo omwetsela mafuta.

ZIMENE MUNGACITE: Kugwila nchito mwakhama kumakhala kosangalatsa mukamaganizila mmene kumapindulitsila ena.​—Mac. 20:35; w15 2/1 5 ¶4-6.

2. Kufufuza Cuma Cauzimu

(Mph. 10)

  • Miy. 12:16​—Kodi mfundo ya palembali ingathandize bwanji munthu akamakumana ndi mavuto? (ijwyp-CN nkhani 95 ¶10-11)

  • Pa kuwelenga Baibulo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?

3. Kuwelenga Baibulo

(Mph. 4) Miy. 12:​1-20 (th phunzilo 5)

CITANI KHAMA PA ULALIKI

4. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 2) KUNYUMBA NDI NYUMBA. (lmd phunzilo 1 mfundo 4)

5. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 3) KUNYUMBA NDI NYUMBA. M’pempheni kuti muziphunzila naye Baibulo. (lmd phunzilo 5 mfundo 4)

6. Kubwelelako

(Mph. 3) ULALIKI WAMWAYI. Onetsani webusaiti yathu kwa munthu amene ali ndi ana. (lmd phunzilo 9 mfundo 3)

7. Kufotokoza Zimene Mumakhulupilila

(Mph. 3) Citsanzo. ijwfq nkhani 3​—Mutu: Kodi Mumakhulupilila Kuti Cipembedzo Canu Cokha Ndiye Coona? (lmd phunzilo 4 mfundo 3)

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Nyimbo 21

8. Yehova Angatithandize Tikamakumana Ndi Mavuto Azacuma

(Mph. 15) Kukambilana.

Kodi mumada nkhawa cifukwa cosowa nchito, kapena poganiza kuti nchito yanu ingathe? Kapenanso mumaona kuti simupeza ndalama zokwanila zokuthandizani pali pano kapena mukadzakalamba? Mavuto azacuma m’dzikoli amabwela mosayembekezeleka. Komabe, Yehova amatitsimikizila kuti ngati taika cifunilo cake patsogolo, nthawi zonse iye adzatipatsa zimene timafunikila. Adzacita zimenezi ngakhale titakumana ndi mavuto azacuma mosayembekezela.​—Sal. 46:​1-3; 127:2; Mat. 6:​31-33.

Cithunzi ca m’vidiyo yakuti “Yehova Sanatigwilitsepo Mwala.” M’bale Alvarado wagwila dzanja la mkazi wake pamene akupemphela ndi banja lawo.

Tambitsani VIDIYO yakuti Yehova Sanatigwilitsepo Mwala. Kenako funsani omvela kuti:

  • Kodi mwaphunzilapo ciyani pa zimene zinacitikila m’bale Alvarado?

Welengani 1 Timoteyo 5:8. Kenako funsani omvela kuti:

  • Kodi lembali lalimbitsa bwanji cikhulupililo canu cakuti Yehova sadzalephela kupatsa alambili ake zimene amafunikila?

Onani mfundo zingapo za m’Baibulo zimene zingakuthandizeni mukakumana ndi mavuto azacuma:

  • Muzikhala umoyo wosalila zambili, ndipo muzipewa nkhongole zosafunikila komanso kugula zinthu zosafunikila. ​—Mat. 6:22

  • Sankhani nchito komanso maphunzilo amene angakupatseni mpata kuti muziika zinthu zauzimu patsogolo.​—Afil. 1:​9-11

  • Muzikhala odzicepetsa komanso okonzeka kusintha. Ngati mungacotsedwe nchito, muzikhala okonzeka kugwila nchito iliyonse imene ingakuthandizeni kupeza zofunikila za banja lanu, ngakhale yooneka yotsika.​—Miy. 14:23

  • Muzikhala okonzeka kugawilako ena zomwe muli nazo, ngakhale ngati inunso muli ndi zocepa.​—Aheb. 13:16

9. Phunzilo la Baibulo la Mpingo

(Mph. 30) bt mutu 26 ¶1-8, mabokosi pa masamba 204, 208

Mawu Othela (Mph. 3) | Nyimbo 57 ndi Pemphelo

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani