MAY 12-18
MIYAMBO 13
Nyimbo 34 ndi Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)
1. Musapusitsidwe ndi “Nyale ya Anthu Oipa”
(Mph. 10)
Anthu oipa alibe ciyembekezo ca tsogolo labwino (Miy. 13:9; w03-CN 9/15 24 ¶5-6)
Musamagwilizane ndi anthu amene angacititse kuti muziona zinthu zoipa ngati zabwino (Miy. 13:20; w12-CN 7/15 12 ¶3)
Yehova amadalitsa munthu wolungama (Miy. 13:25; w04-CN 7/15 31 ¶6)
Umoyo wa anthu amene amafunafuna zinthu za m’dzikoli sukhaladi wacimwemwe ngati mmene umaonekela. Koma anthu amene amacita zimene Yehova amafuna amakhala ndi umoyo wabwino zedi
2. Kufufuza Cuma Cauzimu
(Mph. 10)
Miy. 13:24—Kodi lembali litiphunzitsa ciyani pa nkhani yoonetsa cikondi komanso kupeleka cilango? (w08-CN 4/1 14 ¶4)
Pa kuwelenga Baibulo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?
3. Kuwelenga Baibulo
(Mph. 4) Miy. 13:1-17 (th phunzilo 10)
4. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 3) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Yambani mwa kukambilana nkhani imene ili m’kamwam’kamwa, kenako onetsani munthuyo mfundo ya m’Baibulo imene angagwilizane nayo. (lmd phunzilo 2 mfundo 5)
5. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 4) ULALIKI WAMWAYI. Itanilani munthuyo ku msonkhano. (lmd phunzilo 2 mfundo 3)
6. Nkhani
(Mph. 5) lmd zakumapeto A mfundo 9—Mutu: Ana Amene Amalemekeza Makolo Awo ndi Kuwamvela, Zinthu Zimawayendela Bwino. (th phunzilo 16)
Nyimbo 77
7. “Kuwala Kwa Nyale ya Anthu Olungama Kukuwonjezeka Kwambili”
(Mph. 8) Kukambilana.
M’mawu a Mulungu muli nzelu zabwino koposa. Tikamawadalila kuti atitsogolele pa umoyo wathu, timakhala ndi umoyo wabwino komanso wacimwemwe. Dziko silingathe kutipatsa zinthu zimenezi.
Tambitsani VIDIYO YAKUTI Dzikoli Siingakupatse Zimene Ilibe. Kenako funsani omvela kuti:
Kodi nkhani ya mlongo Gainanshina ionetsa bwanji kuti “nyale ya anthu olungama” ndi yabwino kuposa “nyale ya anthu oipa”?—Miy. 13:9
Musamataye nthawi yanu kulakalaka zinthu za m’dzikoli, kapena kudziimba mlandu cifukwa ca zisankho zimene munapanga kuti mutumikile Yehova. (1 Yoh. 2:15-17) M’malomwake, muziganizila kwambili nzelu zimene munapeza ‘zomwe n’zamtengo wapatali kwambili.’—Afil. 3:8.
8. Zofunikila za Mpingo
(Mph. 7)
9. Phunzilo la Baibulo la Mpingo
(Mph. 30) bt mutu 26 ¶9-17