JUNE 30–JULY 6
MIYAMBO 20
Nyimbo 131 ndi Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)
1. Mmene Mungakhalile pa Cibwenzi Copambana
(Mph. 10)
Muziganizila mmene Yehova amaonela cibwenzi (Miy. 20:24, 25; w24.05 26-27 ¶3-4)
Muyang’anileni capatali munthuyo musanayambe naye cibwenzi (Miy. 20:18; w24.05 22 ¶8)
Dziwanani bwino muli pa cibwenzi (Miy. 20:5; w24.05 28 ¶7-8)
KUMBUKILANI: Si nthawi zonse pamene cibwenzi copambana cimatsogolela ku ukwati. Nthawi zina cisankho canzelu cingakhale kuthetsa cibwenzico.
2. Kufufuza Cuma Cauzimu
(Mph. 10)
Miy. 20:15—Kodi milomo yathu ndi yamtengo wapatali kuposa golide m’lingalilo lotani? (g-CN 5/11 19 ¶1-2)
Pa kuwelenga Baibulo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?
3. Kuwelenga Baibulo
(Mph. 4) Miy. 20:1-15 (th phunzilo 5)
4. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 4) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Munthuyo wakuuzani kuti anasamukila m’dziko lanu kucoka ku dziko lina caposacedwa. (lmd phunzilo 3 mfundo 3)
5. Kubwelelako
(Mph. 4) ULALIKI WAPOYELA. Uzani munthuyo za JW Library®, ndipo muonetseni mmene angaicitile daunilodi pa cipangizo cake. (lmd phunzilo 9 mfundo 5)
6. Kufotokoza Zimene Mumakhulupilila
(Mph. 4) Citsanzo. Ijwbq-CN nkhani 159—Mutu: Kodi Zinyama Zimapita Kumwamba? (lmd phunzilo 3 mfundo 4)
Nyimbo 78
7. Limbikitsani Ena Kuyamba Kuphunzila Nafe Baibulo
(Mph. 5) Kukambilana.
Kuyambitsa maphunzilo a Baibulo ndi mbali yofunika kwambili ya utumiki wathu. Zili conco cifukwa sitingathandize anthu kukhala ophunzila ngati sitiphunzila nawo Baibulo. (Aroma 10:13-15) Pa ulaliki wa kunyumba ndi nyumba, bwanji osadziikila colinga coti muzipempha anthu kuti muziphunzila nawo Baibulo? Coyamba, yesani kupeza nkhani imene mwininyumba angacite nayo cidwi. Kenako, muonetseni mmene phunzilo la Baibulo lingayankhile mafunso ake komanso mmene lingamuthandizile m’njila zina.
Mbali yakuti “Yambani Kuphunzila Baibo” ya pa jw.org, ingakuthandizeni kupempha anthu amene mwakumana nawo kuti muyambe kuphunzila nawo Baibulo.
Kodi mbali yakuti “Yambani Kuphunzila Baibo” ingakuthandizeni bwanji popempha munthu kuti muyambe kuphunzila naye Baibulo?
Kodi ndi njila ziti zimene mwaona kuti ndi zothandiza poyambitsa maphunzilo a Baibulo kwanuko?
8. Vidiyo ya Zimene Gulu Lakwanitsa Kucita ya June
(Mph. 10) Tambitsani VIDIYO.
9. Phunzilo la Baibulo la Mpingo
(Mph. 30) bt mutu 28 ¶8-15