JULY 7-13
MIYAMBO 21
Nyimbo 98 ndi Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)
1. Malangizo Anzelu Othandiza Kuti Ukwati Ukhale Wacimwemwe
(Mph. 10)
Musafulumile kukwatilana ndi munthu musanamudziwe bwino (Miy. 21:5; w03-CN 10/15 4 ¶5)
Muzikhala odzicepetsa pakabuka mikangano (Miy. 21:2, 4; g-CN 7/08 7 ¶2)
Muzicitilana zinthu moleza mtima komanso mokoma mtima (Miy. 21:19; w06-CN 9/15 28 ¶13)
2. Kufufuza Cuma Cauzimu
(Mph. 10)
Miy. 21:31—Kodi vesili litithandiza bwanji kumvetsa ulosi wa pa Chivumbulutso 6:2? (w05-CN 1/15 17 ¶9)
Pa kuwelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?
3. Kuwelenga Baibo
(Mph. 4) Miy. 21:1-18 (th phunzilo 5)
4. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 3) KUNYUMBA NDI NYUMBA. (lmd phunzilo 3 mfundo 3)
5. Kubwelelako
(Mph. 4) ULALIKI WAMWAYI. (lmd phunzilo 7 mfundo 3)
6. Kufotokoza Zimene Mumakhulupilila
(Mph. 5) Citsanzo. ijwfq nkhani 54—Mutu: Kodi a Mboni za Yehova Amaiona Bwanji Nkhani Yothetsa Ukwati? (lmd phunzilo 4 mfundo 3)
Nyimbo 132
7. Muzilemekeza Mnzanu wa mu Ukwati
(Mph. 15) Kukambilana.
Pa tsiku la ukwati, munalumbila pamaso pa Yehova kuti mudzamukonda mnzanu wa mu ukwati ndi kumulemekeza. Conco mmene mumacitila zinthu ndi mwamuna wanu kapena mkazi wanu zimakhudza ubale wanu ndi Yehova.—Miy. 20:25; 1 Pet. 3:7.
Tambitsani VIDIYO yakuti Kuti Banja Likhale Lacimwemwe: Onetsani Ulemu. Kenako funsani omvela kuti:
N’cifukwa ciyani kulemekeza mnzanu wa mu ukwati n’kofunika?
Kodi mungafunike kupanga masinthidwe otani kuti muzilemekezana kwambili?
Kodi ndi mfundo za m’Baibo ziti zimene zingakuthandizeni?
Kodi mungaonetse ulemu kwa mnzanu wa mu ukwati m’njila ziti?
Kodi muyenela kumaganizila zinthu ziti zimene mnzanu wa mu ukwati amacita, ndipo n’cifukwa ciyani?
8. Phunzilo la Baibo la Mpingo
(Mph. 30) bt mutu 28 ¶16-22