JULY 14-20
MIYAMBO 22
Nyimbo 79 ndi Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)
1. Malangizo Anzelu Othandiza Polela Ana
(Mph. 10)
Konzekeletsani ana anu kaamba ka zovuta za pa umoyo (Miy. 22:3; w20.10 27 ¶7)
Yambani kuwaphunzitsa akangobadwa (Miy. 22:6; w19.12 26 ¶17-19)
Muziwalangiza m’njila yacikondi (Miy. 22:15; w06-CN 4/1 9 ¶4)
2. Kufufuza Cuma Cauzimu
(Mph. 10)
Miy. 22:29—Kodi mwambi umenewu tingaugwilitsile nchito bwanji pa zimene timacita mu mpingo, nanga padzakhala mapindu otani? (w21.08 22 ¶11)
Pa kuwelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?
3. Kuwelenga Baibo
(Mph. 4) Miy. 22:1-19 (th phunzilo 10)
4. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 3) KUNYUMBA NDI NYUMBA. (lmd phunzilo 5 mfundo 4)
5. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 4) ULALIKI WAMWAYI. Muonetseni mopezela nkhani zothandiza kwa makolo pa jw.org. (lmd phunzilo 1 mfundo 4)
6. Nkhani
(Mph. 5) ijwyp nkhani 100—Mutu: Kodi Ndingatani Ngati Sindinamvele Lamulo la Makolo Anga? (th phunzilo 20)
Nyimbo 134
7. Khalani Oleza Mtima, Koma Musamalekelele Makhalidwe Oipa
(Mph. 15) Kukambilana.
Kulela ana kumafuna kukhala woleza mtima. Nthawi zonse makolo ayenela kumawamvetsela ana awo ndi kumapatula nthawi yokwanila yoceza nawo. (Deut. 6:6, 7) Pofuna kudziwa zimene zili mumtima mwa ana awo, makolo ayenela kumawafunsa mafunso ndi kumvetsela mwachelu pamene akufotokoza. (Miy. 20:5) Makolo angafunike kubweleza malangizo awo nthawi zambili kuti ana awo awamvetsetse ndi kuwagwilitsa nchito.
Koma izi sizitanthauza kuti makolo oleza mtima amalekelela makhalidwe oipa. Yehova anapatsa makolo mphamvu zoikila ana awo malile a zimene angacite ndi kuwapatsa cilango cofunikila akaphwanya malamulo.—Miy. 6:20; 23:13.
Welengani Aefeso 4:31. Kenako funsani omvela kuti:
N’cifukwa ciyani makolo sayenela kukhala okwiya pamene akupeleka cilango kwa ana awo?
Welengani Agalatiya 6:7. Kenako funsani omvela kuti:
N’cifukwa ciyani m’pofunika kuti makolo azithandiza ana awo kudziwa kuti ngati acita zoipa adzakumana ndi mavuto?
Tambitsani VIDIYO YAKUTI ‘Moleza Mtima, Pitilizani Kulolelana m’Cikondi’—Ana Anu. Kenako funsani omvela kuti:
Kodi mwaphunzila ciyani mu vidiyo iyi?