AUGUST 25-31
MIYAMBO 28
Nyimbo 150 ndi Pemphelo | Mawu Oyamba(Mph. 1)
1. Kusiyana Pakati pa Munthu Woipa ndi Munthu Wolungama
(Mph. 10)
Munthu woipa ndi wamantha koma wolungama amakhala wolimba mtima (Miy. 28:1; w93-CN 5/15 26 ¶2)
Munthu woipa sangapange zisankho zanzelu koma wolungama amatha kupanga zisankho zanzelu (Miy. 28:5; it-2-E 1139 ¶3)
Munthu wolungama amene ndi wosauka ali bwino kuposa munthu woipa amene ndi wolemela (Miy. 28:6; it-1-E 1211 ¶4)
2. Kufufuza Cuma Cauzimu
(Mph. 10)
Miy. 28:14—Kodi mwambi uwu ukuticenjeza za ciyani? (w01-CN 12/1 11 ¶3)
Pa kuwelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?
3. Kuwelenga Baibo
(Mph. 4) Miy. 28:1-17 (th phunzilo 10)
4. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 3) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Kambilanani mmene nkhondo ndi ciwawa zidzathele. (lmd phunzilo 5 mfundo 5)
5. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 3) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Kambilanani mmene nkhondo ndi ciwawa zidzathele. (lmd phunzilo 5 mfundo 4)
6. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 2) ULALIKI WAPOYELA. Kambilanani mmene nkhondo ndi ciwawa zidzathele. (lmd phunzilo 1 mfundo 4)
7. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 3) ULALIKI WAMWAYI. Kambilanani mmene nkhondo ndi ciwawa zidzathele. (lmd phunzilo 2 mfundo 4)
Nyimbo 112
8. Kodi Mumadana ndi Ciwawa?
(Mph. 6) Kukambilana.
Amene anayambitsa ciwawa ndi Satana Mdyelekezi, mdani wamkulu wa Mulungu, yemwe Yesu anamuchula kuti “wakupha.” (Yoh. 8:44) Angelo ena atagwilizana ndi Satana n’kupandukila Mulungu, dziko lapansi linadzadza ndi ciwawa moti Mulungu anaona kuti linali litaipa. (Gen. 6:11) Masiku anonso dzikoli ladzala ndi ciwawa. Pamene mapeto akuyandikila, anthu oopsa komanso osadziletsa akuculukilaculukila.—2 Tim. 3:1, 3.
Welengani Salimo 11:5. Kenako funsani omvela kuti:
Kodi Yehova amawaona bwanji anthu aciwawa, ndipo n’cifukwa ciyani?
Kodi masewela komanso zosangalatsa za masiku ano zimaonetsa bwanji kuti anthu amakonda zaciwawa?
Welengani Miyambo 22:24, 25. Kenako funsani omvela kuti:
Kodi zosangalatsa zimene timasankha komanso anthu amene timaceza nawo zingakhudze bwanji mmene timaonela zaciwawa?
Kodi zosangalatsa zimene timasankha zingaonetse bwanji kuti timakonda zaciwawa?
9. Kampeni Yapadela mu September
(Mph. 9)
Nkhani yokambidwa ndi woyang’anila utumiki. Limbikitsani ofalitsa kutengako mbali mokwanila pa kampeniyi, ndipo fotokozani zimene mpingo wakonza.
Tambitsani VIDIYO yakuti Mtendele Wosatha Pamapeto Pake! (Nyimbo ya Pamsonkhano Wacigawo wa 2022)
10. Phunzilo la Baibo la Mpingo
(Mph. 30) rr mutu 2 ¶19-27