AUGUST 18-24
MIYAMBO 27
Nyimbo 102 ndi Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)
1. Mmene Timapindulila Tikakhala ndi Mabwenzi Enieni
(Mph. 10)
Mabwenzi enieni amalimba mtima kutipatsa uphungu wofunikila (Miy. 27:5, 6; w19.09 5 ¶12)
Mabwenzi enieni angathe kutithandiza bwino kwambili kuposa acibale athu (Miy. 27:10; it-2-E 491 ¶3)
Mabwenzi enieni amatithandiza kukhala anthu abwino (Miy. 27:17; w23.09 10 ¶7)
2. Kufufuza Cuma Cauzimu
(Mph. 10)
Miy. 27:21—Kodi zimene timacita tikatamandidwa zimaonetsa bwanji mmene umunthu wathu ulili? (w06-CN 9/15 19 ¶12)
Pa kuwelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?
3. Kuwelenga Baibo
(Mph. 4) Miy. 27:1-17 (th phunzilo 5)
4. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 3) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Munthuyo si wacipembedzo ca Cikhristu. (lmd phunzilo 6 mfundo 5)
5. Kubwelelako
(Mph. 4) ULALIKI WAMWAYI. Gwilitsani nchito vidiyo ya m’thuboksi yathu. (lmd phunzilo 8 mfundo 3)
6. Nkhani
(Mph. 5) ijwyp nkhani 75—Mutu: Ndingatani Ngati Mnzanga Atandikhumudwitsa? (th phunzilo 14)
Nyimbo 109
7. “M’bale Amene Anabadwa Kuti Akuthandize Pakagwa Mavuto”
(Mph. 15) Kukambilana.
Yehova watipatsa gulu la abale la padziko lonse mmene tingapezemo mabwenzi acikondi. Ngakhale kuti tingakhale ndi mabwenzi ambili mumpingo, kodi ndi angati omwe ndi mabwenzi athu apamtima? Ubwenzi umalimba ngati pali kumvetsetsana, kudalilana, kukambilana mocokela pansi pamtima, kucitila zinthu pamodzi, komanso ngati ticita zinthu mosadzikonda. Conco, kulimbitsa ubwenzi wathu ndi ena kumafuna nthawi komanso khama.
Welengani Miyambo 17:17. Kenako funsani omvela kuti:
N’cifukwa ciyani n’canzelu kulimbitsa ubwenzi wathu ndi ena palipano cisautso cacikulu cisanayambe?
Welengani 2 Akorinto 6:12, 13. Kenako funsani omvela kuti:
Kodi kugwilitsila nchito mfundo ya pa lembali kungatithandize bwanji kupanga mabwenzi?
Tambitsani VIDIYO yakuti “Ciliconse Cili Ndi Nthawi Yake”—Kulimbitsa Ubwenzi Kumatenga Nthawi. Kenako funsani omvela kuti:
Kodi vidiyo iyi yakuphunzitsani ciyani pa nkhani ya kulimbitsa ubwenzi?
Ubwenzi uli ngati mbewu imene imafuna kuithilila komanso nthawi yoti ikule. Mungayambitse ubwenzi mwa kumwetulila, kupeleka moni mwansangala, komanso kuwaonetsa cidwi anthu ena. Ndiyeno pang’onom’pang’ono ubwenziwo umakula pamene mupeza nthawi yoceza. Zotulukapo zake n’zakuti mungapange ubwenzi umene ungakhalepo kwamuyaya.
8. Phunzilo la Baibo la Mpingo
(Mph. 30) rr mutu 2 ¶10-18