SEPTEMBER 1-7
MIYAMBO 29
Nyimbo 28 ndi Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)
1. Pewani Miyambo ndi Zikhulupililo Zosagwilizana ndi Malemba
(Mph. 10)
Muzimvela Yehova ndipo mudzakhala ndi cimwemwe ceniceni (Miy. 29:18; wp16.6 6, bokosi)
Pemphani Yehova kuti akupatseni nzelu zokuthandizani kudziwa ngati mwambo winawake ndi wovomelezeka kwa iye (Miy. 29:3a; w19.04 17 ¶13)
Muzikana ngati anthu ena akukukakamizani kucita nawo miyambo yosagwilizana ndi Malemba (Miy. 29:25; w18.11 11 ¶12)
Kufufuza Malemba mosamala komanso kukamba mwaulemu kungatithandize kuti tisagonje ena akatikakamiza kucita zinthu zosagwilizana ndi Malemba.
2. Kufufuza Cuma Cauzimu
(Mph. 10)
Miy. 29:5—N’cifukwa ciyani tiyenela kuyamikila ena mocokela pansi pa mtima? (w17.10 9 ¶11)
Pa kuwelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?
3. Kuwelenga Baibo
(Mph. 4) Miy. 29:1-18 (th phunzilo 5)
4. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 3) ULALIKI WAMWAYI. Itanilani munthuyo ku nkhani yapadela yotsatila. (lmd phunzilo 2 mfundo 3)
5. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 4) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Gwilitsani nchito Nsanja ya Mlonda Na. 1 2025 poyambitsa makambilano. Sinthani ulaliki wanu ngati munthuyo waonetsa cidwi ndi nkhani inayake yosiyana ndi imene munakonzekela. (lmd phunzilo 3 mfundo 3)
6. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 5) ULALIKI WAMWAYI. Gawilani Nsanja ya Mlonda Na. 1 2025 kwa munthu amene waonetsa kuti ali ndi nkhawa cifukwa ca nkhondo. (lmd phunzilo 3 mfundo 4)
Nyimbo 159
7. Zofunikila za Mpingo
(Mph. 15)
8. Phunzilo la Baibo la Mpingo
(Mph. 30): rr mutu 2 ¶28-31 komanso mabokosi 2A ndi 2B