NOVEMBER 3-9
NYIMBO YA SOLOMO 1-2
Nyimbo 132 ndi Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)
1. Nkhani Yokhudza Cikondi Ceniceni
(Mph. 10)
[Onetsani VIDIYO yakuti Mfundo Zokhudza Buku la Nyimbo ya Solomo.]
Solomo anatamanda kwambili mtsikana wa Cisulami ndipo anamulonjeza kuti adzamupatsa zinthu za mtengo wapatali (Nyimbo 1:9-11)
Cikondi cosatha cimene mtsikana wa Cisulami anali naco pa m’busa n’cimene cinamuthandiza kukhalabe wokhulupilika (Nyimbo 2:16, 17; w15 1/15 30 ¶9-10)
ZIMENE MUNGACITE: Pamene mukuwelenga buku la Nyimbo ya Solomo, gwilitsani nchito mbali yakuti “Zimene Zili m’Buku Lino” mu Baibulo la Dziko Latsopano kuti mudziwe amene akulankhula.
2. Kufufuza Cuma Cauzimu
(Mph. 10)
Nyimbo 2:7—N’cifukwa ciyani mtsikana wa Cisulami ndi citsanzo cabwino kwa Akhristu amene ndi mbeta? (w15 1/15 31 ¶11)
Pa kuwelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?
3. Kuwelenga Baibo
(Mph. 4) Nyimbo 2:1-17 (th phunzilo 12)
4. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 3) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Kambilanani naye imodzi mwa mfundo za coonadi zopezeka pa zakumapeto A m’kabuku ka Kondani Anthu. (lmd phunzilo 1 mfundo 3)
5. Kubwelelako
(Mph. 4) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Kambilanani naye imodzi mwa mfundo za coonadi zopezeka pa zakumapeto A m’kabuku ka Kondani Anthu. (lmd phunzilo 9 mfundo 3)
6. Kupanga Ophunzila
Nyimbo 46
7. “Munthu Wowolowa Manja Adzadalitsidwa”
(Mph. 15) Nkhani yokambilana yokambidwa ndi Mkulu.
Tikamagwilitsa nchito nthawi yathu, mphamvu zathu, ndi zinthu zathu pothandiza ena mowolowa manja timadalitsidwa. Munthu amene walandila thandizo lathu amakhala wosangalala, ndipo nafenso timadalitsidwa cifukwa ca kuolowa manja kwathu. (Miy. 22:9) Tikakhala owolowa manja timakhala acimwemwe podziwa kuti tikutengela citsanzo ca Yehova, ndipo iye adzakondwela nafe.—Miy. 19:17; Yak. 1:17.
Onetsani VIDIYO yakuti Kupatsa Kumabweletsa Cimwemwe. Kenako funsani omvela kuti:
Kodi anthu a mu vidiyoyi apeza bwanji cimwemwe cifukwa ca zopeleka za abale ndi alongo kuzungulila dziko lonse?
Nanga apeza bwanji cimwemwe cifukwa copatsa ena mowolowa manja?
8. Phunzilo la Baibo la Mpingo
(Mph. 30) rr mutu 6 ¶1-6 ndi vidiyo ya zimene zili mmutu 6