NOVEMBER 10-16
NYIMBO YA SOLOMO 3-5
Nyimbo 31 ndi Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)
1. Kukongola kwa Umunthu Wamkati N’kofunika Kwambili
(Mph. 10)
Zokamba za mtsikana wa Cisulami zinaonetsa kukongola kwa umunthu wake wamkati (Nyimbo 4:3, 11; w15 1/15 30 ¶8)
Khalidwe lake loyela analiyelekezela ndi munda wokongola kwambili (Nyimbo 4:12; w00-CN 11/1 11 ¶17)
Kukhala ndi makhalidwe abwino n’kofunika kwambili kuposa kukhala wokongola, ndipo tonse tingathe kukhala ndi makhalidwe amenewa (g04-CN 12/22 9 ¶2-5)
DZIFUNTSENI KUTI, ‘Kodi ndi makhalidwe ati amene ndimakonda kwambili mwa ena?’
2. Kufufuza Cuma Cauzimu
(Mph. 10)
Nyimbo 3:5—N’cifukwa ciyani “ana aakazi a ku Yerusalemu” anawalumbilitsa “pali insa ndiponso pali mphoyo zakuchile”? (w06-CN 11/15 18 ¶4)
Pa kuwelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?
3. Kuwelenga Baibo
(Mph. 4) Nyimbo 4:1-16 (th phunzilo 2)
4. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 3) KUNYUMBA NDI NYUMBA. M’pempheni kuti muyambe kuphunzila naye Baibo. (lmd phunzilo 6 mfundo 4)
5. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 4) ULALIKI WAMWAYI. Muonetseni mmene angapezele nkhani m’cinenelo cake pa jw.org. (lmd phunzilo 4 mfundo 3)
6. Nkhani
(Mph. 5) ijwbq nkhani 131—Mutu: Kodi Baibo Imati Ciyani pa Nkhani Yophauda Komanso Kuvala Zodzikongoletsela? (th phunzilo 1)
Nyimbo 36
7. Kukwatila Kokha mwa Ambuye (Gen. 28:2)
(Mph. 8)
8. Kodi Mudzakhala Mwamuna Kapena Mkazi Wabwino?
(Mph. 7) Kukambilana.
Kodi mukufunafuna munthu womanga naye banja? Kodi ndi makhalidwe ati amene mumafuna mwa munthu amene mukufuna kumanga naye banja? Kodi Akhristu ena amene nawonso akufunafuna munthu womanga naye banja amaona kuti muli ndi makhalidwe abwino? Nthawi zina, munthu angamacite zinthu monga wauzimu, koma m’kupita kwa nthawi umunthu wake wamkati umaonekela.
Lembani lemba logwilizana ndi khalidwe lililonse limene munthu wauzimu amaonetsa.
Kukonda Yehova ndi kumukhulupilila
Kukhala mutu wa banja wabwino kapena kukhala mkazi wogonjela
Wosadzikonda komanso wodzimana
Woganiza bwino komanso wololela
Wakhama komanso wolimbikila pa nchito
9. Phunzilo la Baibo la Mpingo
(Mph. 30) rr mutu 6 ¶7-13 ndi bokosi 6A