LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w20 November masa. 8-11
  • Madalitso Oculuka kwa Amene Amabwelela ku Dziko la Kwawo

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Madalitso Oculuka kwa Amene Amabwelela ku Dziko la Kwawo
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2020
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • “KUMALO AMENE ‘NSOMBA ZIMADYELA’”
  • CIMWEMWE COPEZA ANA AUZIMU
  • YEHOVA ANATICILIKIZA
  • CIMWEMWE COBWELA POTHANDIZA ANTHU KUDZIPATULILA KWA YEHOVA
  • “TINACITA ZIMENE TINAFUNIKILA KUCITA”
  • “Naphunzila Zambili kwa Ena!”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2021
  • Nakhala na Umoyo Wosangalatsa Potumikila Yehova
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • Anadzipeleka Na Mtima Wonse
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
  • Njila Zowonjezela Utumiki Wanu
    Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2020
w20 November masa. 8-11
M’bale Onésime na mlongo Géraldine akulalikila wogulitsa malonda.

M’bale Onésime na mlongo Géraldine

Madalitso Oculuka kwa Amene Amabwelela ku Dziko la Kwawo

ABALE na alongo ambili amene kumbuyoku anasamukila ku maiko olemela, anabwelela ku maiko a kwawo. Cifukwa ca cikondi cawo pa Yehova komanso pa anthu, iwo apita kumadela kumene kukufunikila ofalitsa Ufumu woonjezeleka. (Mat. 22:37-39) Kodi iwo anadzimana ciani, nanga apeza madalitso otani? Kuti tidziŵe, tiyeni tikambilane za dziko la Cameroon, kumadzulo kwa Africa.

“KUMALO AMENE ‘NSOMBA ZIMADYELA’”

Mu 1998, m’bale Onésime anasamuka m’dziko la kwawo la Cameroon. Kwa zaka 14 anakhala ku dziko lakunja. Tsiku lina pa misonkhano yacikhristu, iye anamvela fanizo lokhudza nchito yolalikila. M’nkhaniyo mkambi anati: “Ngati mabwenzi aŵili aŵedza nsomba pamalo osiyana, ndipo mmodzi wa iwo ali pamalo amene nsomba zikudyela kwambili, kodi mnzakeyo amene wagwila tunsomba tocepa sangapite pamalo amene winayo akugwila nsomba zambili?”

Fanizo limeneli linapangitsa Onésime kuganizila zobwelela ku Cameroon kumene anthu ambili anali kufuna kuphunzila Baibo, komanso kukathandiza ofalitsa kumeneko. Koma anali na nkhawa. Kodi adzakwanitsa kujaila umoyo wa m’dziko la kwawo pambuyo pokhala zaka zambili kunja? Kuti aone ngati angakwanitse, iye anapita ku Cameroon kukhalako kwa miyezi 6 cabe. Ndiyeno mu 2012, anasamukilatu.

M’bale Onésime anati: “N’nafunika kujaila nyengo yotentha komanso umoyo wa kumeneko. N’nafunikanso kujaila kukhala pa mabenchi wamba mu Nyumba ya Ufumu.” Anakambanso kuti: “Kuika maganizo pa pulogilamu kunali kunithandiza kuiŵala zamipando yabwino imene tinali kukhalapo mu Nyumba ya Ufumu ku dziko lakunja.”

Mu 2013, m’bale Onésime anakwatila mlongo Géraldine, amene anabwelela ku Cameroon pambuyo pokhala ku France zaka 9. Kodi iwo analandila madalitso otani cifukwa coika zinthu zauzimu patsogolo mu umoyo wawo? M’bale Onésime anati: “Monga banja tinangena Sukulu ya Alengezi a Ufumu na kutumikila pa Beteli. Caka capita, maphunzilo a Baibo okwana 20 a mu mpingo mwathu anabatizika. Apa lomba niona kuti nili kumalo amene ‘nsomba zimadyela.’” (Maliko 1:17, 18) Mlongo Géraldine anawonjezela kuti: “Nalandila madalitso ambili amene sin’nawayembekezele.”

CIMWEMWE COPEZA ANA AUZIMU

Mlongo Judith na m’bale Sam-Castel alalikila munthu ku gombe.

Mlongo Judith na m’bale Sam-Castel

Mlongo Judith anasamukila ku America, koma anali kufuna kucita zambili potumikila Yehova. Iye anati: “Nthawi zonse n’kapita kukacezela banja langa ku Cameroon, pocokako n’nali kulila cifukwa cosiya anthu amene n’nayamba kuphunzila nawo Baibo.” Ngakhale n’conco, mlongo Judith anali kuzengeleza kubwelela ku Cameroon. Iye anali pa nchito ya malipilo abwino, cakuti anali kukwanitsa kutumizila atate ake ndalama za cithandizo ca mankhwala ku Cameroon. Koma podalila Yehova, mlongo Judith anabwelela ku Cameroon. Iye anavomeleza kuti amayewa umoyo wabwino umene anali kukhala ku dziko lakunja. Koma anapemphela kwa Yehova kuti am’thandize kusintha maganizo ake, ndipo analimbikitsidwa kupitila mwa woyang’anila dela na mkazi wake.

Pokumbukila mmene zinthu zinalili, mlongo Judith anati: “M’zaka zitatu zapita, n’napeza ana auzimu anayi.” Mlongo Judith anayamba kutumikila monga mpainiya wapadela. Lomba, amatumikila na mwamuna wake, m’bale Sam-Castel, m’nchito ya m’dela. Nanga n’ciani cinacitika kwa atate ake a mlongo Judith? Iye pamodzi na a m’banja lake, anakwanitsa kupeza cipatala kunja kwa dziko cimene cinati cidzawathandiza kucita opaleshoni atate ake. Cokondweletsa n’cakuti opaleshoni inayenda bwino.

YEHOVA ANATICILIKIZA

Mbale Victor na mlongo Caroline alalikila munthu ku paki.

Mbale Victor na mlongo Caroline

M’bale wina dzina lake Victor anasamukila ku Canada. Pambuyo poŵelenga nkhani yokhudza maphunzilo apamwamba mu Nsanja ya Mlonda, iye anaganizila za maphunzilo amene anali kucita. Analeka maphunzilo ake a ku yunivesiti na kuyamba maphunzilo a nchito zamanja osatenga nthawi yaitali. Iye anati: “Maphunzilo amenewa ananithandiza kupeza nchito mwamsanga, komanso kugwila nchito ya kumtima kwanga ya upainiya. M’kupita kwa nthawi, m’bale Victor anakwatila mlongo Caroline, ndipo onse aŵili anapita kukaceza ku Cameroon. Pamene iwo anayenda kukaona ofesi yanthambi, abale ena kumeneko anawalimbikitsa zoganizila kukatumikila ku Cameroon. M’bale Victor anati: “Tinaona kuti panalibe coletsa, cifukwa tinali kale na umoyo wosalila zambili. Conco tinaona kuti tikhoza kukatumikila kumeneko.” Ngakhale kuti mlongo Caroline anali na mavuto ena okhudza thanzi, iwo anasankhabe kubwelela ku Cameroon.

M’bale Victor na mlongo Caroline anayamba upainiya wanthawi zonse kuti athandize anthu ambili acidwi m’gawo lawo. Ndalama zimene anasunga zinawathandiza kwakanthawi. Pambuyo pake iwo anabwelela ku Canada kukagwilako nchito kwa miyezi ingapo. Izi zinawathandiza kubwelelanso ku Cameroon kukapitiliza upainiya. Kodi anapeza madalitso otani? Iwo analoŵa Sukulu ya Alengezi a Ufumu, anatumikilapo monga apainiya apadela, ndipo tsopano ni atumiki a nchito yomanga. M’bale Victor anati: “Kusiya umoyo wathu wa wofu-wofu, kunatithandiza kuona cicilikizo ca Yehova.”

CIMWEMWE COBWELA POTHANDIZA ANTHU KUDZIPATULILA KWA YEHOVA

Mlongo Stéphanie na m’bale Alain aimilila pa kasitandi ka ulaliki, ndipo akulalikila mzimayi.

Mlongo Stéphanie na m’bale Alain

Mu 2002, m’bale Alain anali kuphunzila pa yunivesiti ku Germany. Anaŵelenga kathilakiti kakuti, Kodi Achinyamata Mukufuna Kuchita Chiyani Pamoyo Wanu? Zimene anaŵelenga zinam’limbikitsa kupanga zolinga zatsopano. Mu 2006, analoŵa Sukulu Yophunzitsa Utumiki, ndipo anatumizidwa kukatumikila ku Cameroon, kumene anabadwila.

Ku Cameroon, m’bale Alain anapeza nchito yoseŵenza maola ocepa. M’kupita kwa nthawi, anapeza nchito ya malipilo abwino, koma anali na nkhawa kuti nchitoyo idzam’pangitsa kucita zocepa mu utumiki. Conco atapemphedwa kutumikila monga mpainiya wapadela, anavomela popanda kuzengeleza. Abwana ake anamuuza kuti adzamuonjezela malipilo, koma m’bale Alain sanasinthe cosankha cake. Pambuyo pake, m’bale Alain anakwatila mlongo Stéphanie, amene anakhala ku France kwa zaka zambili. Kodi iye anakumana na mavuto otani atabwelela ku Cameroon?

Mlongo Stéphanie anati: “N’nayamba kudwala matenda ena ang’ono-ang’ono, koma n’nali kulandila cithandizo ca mankhwala pafupi-pafupi, ndipo n’nali kukhala bwino.” Yehova anadalitsa banjali cifukwa ca kupilila kwawo. M’bale Alain anafotokoza kuti: “Pamene tinapita kukalalikila ku mudzi wina wakutali wochedwa Katé, tinapeza anthu ambiliko ndithu amene anali kufuna kuphunzila Baibo. Pambuyo pake, tinali kuphunzila nawo Baibo kupitila pa foni. Aŵili mwa ophunzila Baibo amenewo anabatizika, ndipo kagulu ka ofalitsa kanakhazikitsidwa. Mlongo Stéphanie anawonjezela kuti: “Palibe cinthu cina cokondweletsa monga kuthandiza anthu kufika podzipatulila kwa Yehova. Cifukwa cotumikila kuno, tapeza cimwemwe cimeneci mobweleza-bweleza.” Lomba, m’bale Alain na mlongo Stéphanie akutumikila m’nchito ya m’dela.

Mapindu a Kutumikila m’Dziko la Kwanu

“Tinali kucidziŵa kale cikhalidwe komanso mmene anthu amaonela zinthu. Anthu sanali kutikaikila kwambili monga mmene zingakhalile kwa anthu acilendo a kudziko lina. Ndipo tinali kukambilana na anthu mosavuta.”—Alain

“Tinali kuyenda kumalo osiyana-siyana mosavuta, ngakhale kumalo kumene zingakhale zovuta kwa alendo ocokela ku maiko ena.”—Stéphanie

“TINACITA ZIMENE TINAFUNIKILA KUCITA”

M’bale Léonce na mlongo Gisèle akulalikila mzimayi pa buliji.

M’bale Léonce na mlongo Gisèle

Mlongo Gisèle anabatizika pamene anali ku sukulu ya zacipatala ku Italy. Iye anacita cidwi na umoyo wosalila zambili wa apainiya aŵili amene anali kum’phunzitsa Baibo, ndipo nayenso anafuna kucita zambili mu utumiki. Conco, mlongo Gisèle anayamba kutumikila monga mpainiya wanthawi zonse pamene anali kutsiliza maphunzilo ake.

Mlongo Gisèle anali kufuna kucita zambili potumikila Yehova kwawo ku Cameroon, koma anali na nkhawa. Iye anati: “N’nafunikila kufafanizitsa cilolezo cokhala m’dziko la Italy, komanso kusiya mabwenzi na acibale ku Italy.” Ngakhale n’telo, mu May 2016, mlongo Gisèle anabwelelabe ku Cameroon. Patapita nthawi, iye anakwatilana na m’bale Léonce, ndipo ofesi yanthambi ya Cameroon inawatumiza kukatumikila ku tauni ya Ayos, kumene kunali kufunikila ofalitsa Ufumu owonjezeleka.

Kodi umoyo unali bwanji ku Ayos? Mlongo Gisèle anasimba kuti: “Nthawi zambili magetsi amapita kwa milungu ingapo, moti mafoni athu amakhala osachajing’a. Nthawi zambili sitinali kuwaseŵenzetsa. N’naphunzila kuphikila pankhuni, ndipo tinali kuyenda na mawilibala komanso matoci popita kukatapa madzi usiku, panthawi imene ku citsime sikunali kukhala anthu ambili.” N’ciani cinathandiza banjali kupilila? Mlongo Gisèle anati: “Mzimu wa Yehova, mwamuna wabwino, cilimbikitso, na thandizo la ndalama locokela kwa acibale komanso mabwenzi, zinatithandiza kupilila.”

Kodi mlongo Gisèle ni wokondwela kuti anabwelela ku dziko la kwawo? “Inde! Mosapeneka konse. N’zoona kuti poyamba panali zovuta zina na nkhawa, koma titagonjetsa zovutazo, ine na mwamuna wanga tinaona kuti tinacita zimene tinafunikila kucita. Timam’dalila Yehova ndipo timaona kuti tili naye pafupi.” Anatelo mlongo Gisèle. M’bale Léonce na mlongo Gisèle anangena Sukulu ya Alengezi a Ufumu, ndipo tsopano akutumikila monga apainiya apadela apakanthawi.

Monga asodzi amene amalimba mtima kuti agwile nsomba zambili ngakhale akumane na zovuta, amene amabwelela ku maiko a kwawo amadzimana zinthu zina kuti akathandize anthu maganizo abwino kumva uthenga wa Ufumu. Mosakaikila, Yehova adzakumbukila nchito za ofalitsa olimbika amenewa, pa cikondi cimene aonetsa pa dzina lake. (Neh. 5:19; Aheb. 6:10) Ngati mumakhala kudziko lakunja, ndipo kudziko la kwanu kufunikila ofalitsa Ufumu owonjezeleka, kodi mungabwelele ku dziko lanu? Mukatelo, madalitso oculuka akukuyembekezelani.—Miy. 10:22.

Kodi Anakwanitsa Bwanji?

Ngati muganizila zobwelela ku dziko la kwanu, mvelani zimene zinathandiza abale na alongo ochulidwa m’nkhani ino.

  • Mungayembekezele ciani?

    “Khalani okonzeka kuti acibale komanso mabwenzi ena adzakuopsezani kuti musabwelele. Koma dalilani Yehova.”—Alain

  • Mungakonzekele bwanji?

    “Panthawiyo n’napemphela kwambili kuposa kale lonse.”—Gisèle

    “N’nasungako ndalama kuti n’sakadalile anthu ena kunipatsa thandizo.”—Géraldine

    “N’napita kwa dokotala kuti atsimikize ngati thanzi langa lili bwino.”—Stéphanie

  • Kodi muzikapeza bwanji zofunikila?

    “Poyamba n’nali kuseŵenzetsa ndalama zimene n’nasunga. Pambuyo pake n’nayamba kuphunzitsa pa sukulu ya sekondale. Patapita nthawi n’naphunzila mopangila sopo n’kumagulitsa.”—Géraldine

    “Tinali kupeza ndalama zina mwa kupanga maswiti amene tinali kuodetsa ku masitolo.”—Gisèle

    “N’nali kugwila nchito yomasulila zinthu kupitila pa intaneti.”—Onésime

  • Mungakhale bwanji wotetezeka?

    “N’napeza malo otetezeka amene anali pafupi na abale na alongo.”—Géraldine

    “Nthawi zonse nimayenda na wina polalikila.”—Gisèle

    “Sin’nali kuyenda nekha usiku. Komanso, sin’nali kunyamula zinthu zodula poyenda.”—Stéphanie

    “Sin’nali kuuza anthu ambili zakuti n’nacokela kunja, ndipo kuti pasakhale kusiyana, n’nali kucita zinthu mofanana na ena onse.”—Judith

  • Mungacite ciani kuti mukhalebe acimwemwe na kupitiliza kubala zipatso?

    “Tinakhala okonzeka kusintha. Sitinali kuiwala cifukwa cimene tinabwelela, ndipo tinali kuika maganizo athu pa zinthu zolimbikitsa.”—Victor

    “N’nafunika kukulitsa khalidwe la kukhala wokhutila.”—Alain

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani