MAWU A M’BAIBO
Kukhululuka Macimo Dipo Lisanapelekedwe
Mulungu amatikhululukila macimo athu kokha kupitila mu nsembe ya dipo ya magazi a Yesu. (Aef. 1:7) Koma Baibo imati: “Mulungu anacita izi pofuna kuonetsa cilungamo cake pokhululuka macimo amene anacitika kale,” kutanthauza Yesu asanapeleke dipo. (Aroma 3:25) Kodi zinatheka bwanji Yehova kucita zimenezi, koma pa nthawi imodzi-modzi akusungabe cilungamo cake?
Yehova atalonjeza kuti adzapeleka “mbewu” imene idzapulumutsa anthu omukhulupilila, kwa Iye zinali ngati nsembe ya dipo yapelekedwa kale. (Gen. 3:15; 22:18) Mulungu anali wotsimikiza ndithu kuti Mwana wake wobadwa yekha adzapeleka dipo mofunitsitsa. (Agal. 4:4; Aheb. 10:7-10) Yesu ali pa dziko lapansi monga woimilako Yehova, anali na mphamvu zokhululukila macimo dipo isanapelekedwe. Anacita zimenezi kwa omwe anam’khulupilila podziŵa kuti dipo limene anali kudzapeleka inali kudzaphimba macimo awo.—Mat. 9:2-6