LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w25 February tsa. 32
  • Onetsani Kulimba Mtima Mukapanikizika

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Onetsani Kulimba Mtima Mukapanikizika
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Nkhani Zofanana
  • Yehova Atumiza Yeremiya Kuti Akalalikile
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • ‘Limba Mtima, Ugwile Nchito Mwamphamvu’
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
w25 February tsa. 32

ZIMENE MUNGACITE PA KUWELENGA KWANU

Onetsani Kulimba Mtima Mukapanikizika

Welengani Yeremiya 38:​1-13 kuti muphunzile mmene mneneli Yeremiya ndi Ebedi-meleki anaonetsela kulimba mtima.

Mvetsani nkhani yonse. Kodi n’cifukwa ciyani Yeremiya anafunika kukhala wolimba mtima polengeza uthenga wa Yehova? (Yer. 27:​12-14; 28:​15-17; 37:​6-10) Kodi anthu anatani atamva uthenga wake?​—Yer. 37:​15, 16.

Kumbani mozamilapo. Kodi anthu anali kukakamiza Yeremiya kucita ciyani? (jr-CN 26-28 ¶20-22) Fufuzani zokhudza zitsime zakale. (it-1-E 471) Kodi muganiza Yeremiya anali kumva bwanji ali m’citsime camatope? Kodi Ebedi-meleki ayenela kuti anali kuopa ciyani?​—w12-CN 5/1 31 ¶2-3.

Onani zimene mwaphunzilapo. Dzifunseni kuti:

  • ‘Kodi nkhaniyi indiphunzitsa ciyani ponena za mmene Yehova amatetezela atumiki ake okhulupilika?’ (Sal. 97:10; Yer. 39:​15-18)

  • ‘Kodi ndi pa zocitika ziti pomwe ndingafunike kukhala wolimba mtima?’

  • ‘Ndingacite bwanji kuti ndiwonjezele kulimba mtima kuti ndizicita zoyenela ndikapanikizika?’ (w11-CN 3/1 30)a

a Kuti mudziwe zowonjezela zokhudza zimene mungacite pa kuwelenga kwanu, onani nkhani yakuti “Mfundo Yothandiza pa Kuŵelenga Kwanu” mu Nsanja ya Mlonda ya July 2023.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani