Muzisunga “Umodzi Umene Timaupeza Mothandizidwa ndi Mzimu Woyela”
MTUMWI Paulo analimbikitsa Akhristu a ku Efeso kuti: “Muzilolelana cifukwa ca cikondi. Muziyesetsa ndi mtima wonse kusunga umodzi umene timaupeza mothandizidwa ndi mzimu woyela pokhala, mwamtendele umene uli ngati comangila cimene cimatigwilizanitsa.”—Aef. 4:2, 3.
“Umodzi,” kapena kuti mgwilizano, umene timasangalala nawo “timaupeza mothandizidwa ndi mzimu woyela.” Komabe, monga mmene Paulo ananenela, pafunika khama kuti umodzi usungidwe. Ndani ayenela kucita zimenezi? Kunena zoona, Mkhristu aliyense ayenela kucita mbali yake “posunga umodzi umene timaupeza mothandizidwa ndi mzimu woyela.”
Tiyelekeze kuti munthu wina wakupatsani galimoto yatsopano. Kodi ndani amene ali ndi udindo woisamalila? Yankho n’lodziwikilatu. Ngati galimotoyo yaonongeka cifukwa coti simunaisamalile, simungaimbe mlandu amene anakupatsaniyo.
Mofananamo, ngakhale kuti umodzi ndi mphatso yocokela kwa Mulungu, aliyense wa ife ayenela kuyesetsa kuusungitsa. Ngati tinakhumudwitsana ndi m’bale kapena mlongo winawake, tiyenela kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndikucita mbali yanga posungitsa umodzi umene timaupeza mothandizidwa ndi mzimu woyela mwa kuthetsa nkhaniyo?’
‘MUZIYESETSA NDI MTIMA WONSE’ KUSUNGA MGWILIZANO
Monga mmene Paulo ananenela, nthawi zina tiyenela kucita khama kuti tisunge umodzi umene timapeza mothandizidwa ndi mzimu woyela. Tingafunike kucita zimenezi maka-maka ngati m’bale kapena mlongo watikhumudwitsa. Kodi nthawi zonse pamafunika kuti tikambilane ndi munthu amene watikhumudwitsa kuti tisunge mgwilizano? Osati kweni-kweni. Dzifunseni kuti, ‘Kodi kukambilana nkhaniyi ndi munthu yemwe anandikhumudwitsa kudzasungitsa mgwilizano kapena kudzangoonjezela bvutolo?’ Nthawi zina, cimakhala canzelu kungonyalanyaza nkhaniyo kapena kum’khululukila munthu wolakwayo.—Miy. 19:11; Maliko 11:25.
Dzifunseni kuti, ‘Kodi kukambilana nkhaniyi ndi munthu yemwe anandikhumudwitsa kudzasungitsa mgwilizano kapena kudzangoonjezela bvutolo?’
Mtumwi Paulo anatilimbikitsa kuti tipitilize ‘kulolelana cifukwa ca cikondi.’ (Aef. 4:2) Buku lina linati mauwa angamasulilidwenso kuti “muzibvomeleza mmene alili.” Izi zitanthauza kuti tiyenela kubvomeleza kuti Akhristu anzathu ndi ocimwa monga mmene ifenso tilili. N’zoona kuti tikuyesetsa kubvala “umunthu watsopano.” (Aef. 4:23, 24) Koma palibe angacite zimenezi mwangwilo. (Aroma 3:23) Kudziwa mfundo imeneyi kudzathandiza kuti zikhale zosabvuta kulolelana ndi kukhululukilana. Zimenezi zidzatithandiza “kusunga umodzi umene timaupeza mothandizidwa ndi mzimu woyela.”
Tikamayesetsa kukhululuka ndi kuiwala zimene ena atilakwila, tidzathandiza kuti mumpingo mukhale “mtendele umene uli ngati comangila cimene cimatigwilizanitsa.” Mau acigiriki amene anamasulilidwa kuti “comangila cimene cimatigwilizanitsa” pa Aefeso 4:3 anamasulilidwa kuti “minyewa” pa Akolose 2:19. Minyewa ndi yolimba kwambili ndipo imagwilizanitsa mafupa. Mofananamo, mtendele komanso cikondi cathu pa abale zimatithandiza kuti tikhalebe ogwilizana ngakhale kuti nthawi zina makonda amasiyana.
Conco, Mkhristu mnzathu akatilakwila, tiziyesetsa kuonamo zabwino mwa iye osati zimene amalakwitsa. (Akol. 3:12) Popeza kuti tonsefe ndife opanda ungwilo, inunso panthawi ina muyenela kuti munakhumudwitsapo winawake. Kukumbukila zimenezi kudzakuthandizani kucita mbali yanu posunga “umodzi umene timaupeza mothandizidwa ndi mzimu woyela.”