MAU A M’BAIBO
Kusewenzetsa ‘Mphatso Yanu Yauzimu’
Tonsefe timalimbikitsidwa tikakhala pamodzi ndi abale komanso alongo. Koma kuti nthawi imeneyi izikhaladi yolimbikitsa, pali zina zimene tiyenela kucita. M’Baibo, kulimbitsa cikhulupililo ca wina ndi mnzake kumachedwa “mphatso . . . yauzimu.” (Aroma 1:11, 12) Kodi mphatsoyi tingaigwilitse nchito bwanji mokwanila?
Limbikitsani ena mwa mau anu. Mwacitsanzo, tingalimbikitse ena pamisonkhano mwa kupeleka ndemanga zokamba kwambili za Yehova, Mau ake, ndi anthu ake, osati za ife. Ndipo poceza ndi alambili anzathu, tiyenela kukambilana nkhani zolimbikitsa.
Limbikitsani ena mwa zisankho ndi zocita zanu. Mwacitsanzo, ena apanga cisankho cokhalabe mu utumiki wanthawi zonse ngakhale kuti akukumana ndi mabvuto enaake. Ena amafika pamsonkhano wa mkati mwa mlungu ngakhale kuti amapanikizika ndi nchito, kapena akudwala matenda osathelapo.
Kodi mau ndi zocita zanu zimalimbikitsa abale ndi alongo anu? Ndipo kodi mumakhala chelu kuti muone zimene ena amakamba ndi kucita kuti akulimbikitseni?