NKHANI YA PACIKUTO | NI MPHATSO ITI YOPOSA ZONSE?
“Inali Mphatso Yabwino Koposa Imene Sin’nalandilepo”
Umu ni mmene mtsikana wina wa zaka 13 anakondwelela, atalandila kagalu monga mphatso. Mayi wina wabizinesi anakamba kuti kompyuta imene atate ŵake anamupatsa pamene anali pa sukulu, ni mphatso imene inasintha umoyo wake. Mwamuna wina wa banja lacatsopano, anakamba kuti khadi yokondwelela caka coyamba ca cikwati cawo imene mkazi wake anamukonzela inali mphatso yoposa zonse zimene analandilapo.
Caka ciliconse, anthu amathela nthawi yaitali kusakila mphatso yabwino “koposa” imene angapatse mnzawo, kapena wacibululu wawo pa cocitika capadela. Ndipo ambili amafuna kumva mau monga a kuciyambi kwa nkhani ino kucokela kwa wolandila mphatsoyo. Nanga bwanji imwe? Kodi mungakonde kupeleka kapena kulandila mphatso yabwino kwambili?
Kukhala na colinga cimeneci kungakhale kwabwino kwambili, cifukwa mphatsoyo ingathandize woilandila na kukondweletsa woipeleka. Ndiye cifukwa cake Baibo imati: “Kupatsa kumabweletsa cimwemwe coculuka kuposa kulandila.” (Machitidwe 20:35) Ndipo cimwemwe cimene cimabwela cifukwa copatsa, cimakula kwambili ngati wolandila mphatsoyo waiona kukhala yamtengo wapatali.
Nanga mungacite ciani kuti imwe na munthu amene mwapatsa mphatso mukhale acimwemwe? Ndipo ngati mwalephela kupeleka mphatso yabwino “koposa,” mungacite ciani kuti mphatso imene mwapeleka iyamikilidwe?