ZIMENE MUNGACITE PA KUWELENGA KWANU
Limbitsani Cikhulupililo Canu Cakuti Yehova Ali ndi Mphamvu Zokupulumutsani
Welengani Numeri 13:25–14:4 imene ionetsa kuti Aisiraeli sanali kum’khulupilila Yehova.
Mvetsani nkhani yonse. N’cifukwa ciani Aisiraeli pamene anali kucoka ku Iguputo anali kufunika kukhala ndi cikhulupililo cakuti Yehova ali ndi mphamvu zowapulumutsa? (Sal. 78:12-16, 43-53) N’ciani cinawalepheletsa kum’dalila Yehova? (Deut. 1:26-28) Kodi Yoswa ndi Kalebe anaonetsa bwanji kuti anali kum’dalila Yehova?—Num. 14:6-9.
Kumbani mozamilapo. Kodi Aisiraeli anayenela kutani kuti azim’dalila kwambili Yehova? (Sal. 78:12-16, 43-53) Kodi pali kugwilizana kotani pakati pa kudalila Yehova ndi kum’lemekeza?—Num. 14:11.
Ganizilani zimene mungaphunzilepo. Dzifunseni kuti:
‘Ndi pa zocitika ziti pomwe zingakhale zobvuta kwa ine kudalila Yehova ndi mtima wonse?’
‘Ndingatani kuti ndizim’dalila kwambili Yehova pali pano komanso m’tsogolo?’
‘Cisautso cacikulu cikadzayamba, kodi n’ciani cimene sindiyenela kukaikila ngakhale pang’ono?’—Luka 21:25-28.