Zamkati
September 15, 2015
© 2015 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
NKHANI ZOPHUNZILA
OCTOBER 26, 2015–NOVEMBER 1, 2015
Kodi Mukuyesetsa Kufika pa Ucikulile Umene Kristu Anafikapo?
TSAMBA 3
NOVEMBER 2-8, 2015
Kodi Cikumbumtima Canu n’Codalilika?
TSAMBA 9
NOVEMBER 9-15, 2015
TSAMBA 15
NOVEMBER 16-22, 2015
Kodi Yehova Waonetsa Bwanji Kuti Amatikonda?
TSAMBA 21
NOVEMBER 23-29, 2015
Tingaonetse Bwanji Kuti Timakonda Yehova?
TSAMBA 27
NKHANI ZOPHUNZILA
▪ Kodi Mukuyesetsa Kufika pa Ucikulile Umene Kristu Anafikapo?
▪ Kodi Cikumbumtima Canu n’Codalilika?
M’nkhanizi, tidzaphunzila mmene atumiki a Mulungu angakulitsile ubwenzi wao ndi Yehova n’colinga cakuti akhale Akristu ofikapo. Tidzaphunzilanso mmene tingaphunzitsile cikumbumtima cathu ndi mmene tingacigwilitsile nchito popanga zosankha zanzelu.
▪ “Limbani m’Cikhulupililo”
Nkhani ya Petulo pamene anayenda pa Nyanja ya Galileya ingatiphunzitse zinthu zofunika pankhani ya cikhulupililo. Nkhaniyi idzatithandiza kuona ngati cikhulupililo cathu cayamba kufooka ndi mmene tingacilimbitsile.
▪ Kodi Yehova Waonetsa Bwanji Kuti Amatikonda?
▪ Tingaonetse Bwanji Kuti Timakonda Yehova?
Cikondi cimene Yehova amationetsa ndiponso cikondi cathu pa iye zimatipatsa cimwemwe ceniceni. M’nkhani ziŵilizi, tidzakambilana mmene Yehova amaonetsela cikondi cake pa ife ndi mmene tingaonetsele kuti timam’konda.
PACIKUTO: Ofalitsa a ku Italy amene amasonkhana ndi mpingo wa cinenelo ca Cichaina, akulalikila alendo odzaona malo mumzinda wa Rome. Mwezi uliwonse, anthu ambili amabwela pa mashelufu a mawilo a mabuku athu amene amaikidwa pafupi ndi malo amene pamapitila anthu ambili.
ITALY
KULI ANTHU
60,782,668
OFALITSA
251,650
APAINIYA ANTHAWI ZONSE
33,073
Uthenga wabwino ukulalikidwa m’zinenelo zina 37 ndi ofalitsa oposa 24,000.