Yophunzila
MARCH 2016
NKHANI ZOPHUNZILA MLUNGU WA: MAY 2-29, 2016
© 2016 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
CITHUNZI CA PACIKUTO:
BELGIUM
Nyumba ya Ufumu ya Wijnegem ikumangidwa m’mbali mwa mseu waukulu m’dela la Antwerp. Anthu amene amapita mumseu umenewu amaona cizindikilo ca JW.ORG cimene cakhalapo kucokela pamene anayamba kumanga
KULI ANTHU
11,132,269
OFALITSA
25,839
OPEZEKA PA CIKUMBUTSO (2014)
44,635
Magazini iyi si yogulitsa. Colinga cake ndi kuthandiza pa nchito yophunzitsa Baibulo imene imacitika padziko lonse lapansi. Ndalama zoyendetsela nchitoyi ndi zimene anthu amapeleka mwa kufuna kwao.
Ngati mufuna kupeleka ndalama zocilikizila nchitoyi, pitani pa www.pr2711.com.
Baibulo limene taseŵenzetsa ndi Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika, kusiyapo ngati taonetsa lina. Komabe, masipeling’i a Cinyanja m’magazini ino tatsatila malamulo a m’buku lochedwa A Unified Standard Orthography for South-Central African Languages.