Zamkati
MLUNGU WA MAY 30, 2016–JUNE 5, 2016
3 Mulungu Amakonda Anthu Okhulupilika
Nkhaniyi ifotokoza cimene cinathandiza Yefita ndi mwana wake wamkazi kukhalabe okhulupilika ngakhale panthawi yovuta. Tidzaphunzila cifukwa cake tifunika kudzipeleka kwa Mulungu kuti apitilize kutikonda.
MLUNGU WA JUNE 6-12, 2016
9 “Mulole Kuti Kupilila Kumalize Kugwila Nchito Yake”
Kuti tidzalandile mphatso ya moyo wosatha, tiyenela kupilila mpaka mapeto. Nkhaniyi ifotokoza zinthu zinai zimene zingatithandize kupilila, ndiponso zitsanzo zitatu za anthu okhulupilika amene anapilila. Ifotokozanso nchito imene khalidwe la kupilila liyenela kumaliza mwa aliyense wa ife.
MLUNGU WA JUNE 13-19, 2016
15 N’cifukwa Ciani Tiyenela Kusonkhana?
Pali zinthu zambili zimene zingatilepheletse kusonkhana nthawi zonse. Nkhaniyi itilimbikitsa kuti tipitilize kupezeka pamisonkhano. Ifotokoza cifukwa cake kupezeka pamisonkhano kumatipindulitsa, kumathandiza ena, ndi kukondweletsa Yehova.
MLUNGU WA JUNE 20-26, 2016
21 Pewani Kutenga Mbali m’Ndale za Dziko Loipali
Ngakhale kuti maboma ambili masiku ano amatilola kusatenga mbali m’ndale, tiyenela kuyembekezela kuti adzatikakamiza kutengamo mbali pamene tiyandikila mapeto. M’nkhani ino, tikambilana zinthu zinai zimene zidzatithandiza kukhalabe okhulupilika kwa Yehova.
27 Mbili Yanga—Masisitele Anakhala Paubale Weniweni Wakuuzimu