Yophunzila
APRIL 2016
NKHANI ZOPHUNZILA MLUNGU WA: MAY 30–JUNE 26, 2016
© 2016 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
CITHUNZI CA PACIKUTO:
COLOMBIA
Mboni zimacita zimene zingathe kuti zilalikile uthenga wabwino kwa anthu amene amakamba Ciwayu. Anthu amenewa amakonda kukamba za Mulungu. Nthawi zambili amapita kumzinda kukagulitsa zinthu zokongola zimene amapanga. Kumeneko amamva uthenga wabwino kwa Mboni zimene zimacita ulaliki wa poyela
OFALITSA
166,049
MAPHUNZILO A BAIBULO
229,723
OPEZEKA PA CIKUMBUTSO (2015)
510,217
Magazini iyi si yogulitsa. Colinga cake ndi kuthandiza pa nchito yophunzitsa Baibulo imene imacitika padziko lonse lapansi. Ndalama zoyendetsela nchitoyi ndi zimene anthu amapeleka mwa kufuna kwao.
Ngati mufuna kupeleka ndalama zocilikizila nchitoyi, pitani pa www.pr2711.com.
Baibulo limene taseŵenzetsa ndi Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika, kusiyapo ngati taonetsa lina. Komabe, masipeling’i a Cinyanja m’buku lino tatsatila malamulo a m’buku lochedwa A Unified Standard Orthography for South-Central African Languages.