Pawel Gluza/500Px Plus/Getty Images
KHALANI MASO!
Nyama Zakuchile Zacepa ndi 73 Pelesenti m’Zaka 50—Kodi Baibulo Likutipo Ciyani?
Pa October 9, 2024, bungwe la World Wildlife Fund linapeleka lipoti lodetsa nkhawa loonetsa mmene zocita za anthu zikukhudzila nyama zakuchile. Linanena kuti “m’zaka 50 zapitazo (kucokela mu 1970 kufika mu 2020), ciwelengelo ca nyama zakuchile catsika ndi 73 pelesenti.” Lipotilo linatinso: “Tinganene motsimikiza kuti m’tsogolomu umoyo padziko lapansi udzadalila zimene zicitike m’zaka 5 zikubwelazi.”
M’pomveka kuti anthu ambili ali ndi nkhawa cifukwa ca malipoti amenewa. Timalikonda dziko lapansi lokongolali ndipo cimatiwawa tikaona nyama zakuchile zikuwonongeka. Timamva conco cifukwa Mulungu anatilenga kuti tizisamalila nyama.—Genesis 1:27, 28; Miyambo 12:10.
Mungadzifunse kuti, ‘Kodi tidzakwanitsa kuteteza nyama zakuchile? Kodi Baibulo likutipo ciyani?’
Ciyembekezo ca tsogolo labwino.
Ngakhale titayesetsa bwanji, sitingathe kuteteza nyama padzikoli, koma Mulungu yekha ndi amene angakwanitse kucita zimenezi. Baibulo pa Chivumbulutso 11:18, linakambilatu kuti Mulungu ‘adzawononga amene akuwononga dziko lapansi.’ Vesili limatiphunzitsa zinthu ziwili:
1. Mulungu sadzalola kuti anthu awononge dzikoli kothelatu.
2. Mulungu adzacitapo kanthu posacedwa. Tidziwa bwanji zimenezi? Cifukwa zocita za anthu masiku ano zikuika umoyo wa nyama paciwopsezo cacikulu kuposa n’kale lonse.
Kodi Mulungu adzacita ciyani kuti athetse vuto limeneli? Adzagwilitsa nchito boma lake lakumwamba, kapena kuti Ufumu, polamulila dziko lonse lapansi. (Mateyo 6:10) Boma limenelo lidzaphunzitsa anthu omvela mmene angasamalile nyama komanso kuziteteza.—Yesaya 11:9.