THANDIZO KWA OFEDWA
M’magazini Ino Thandizo Kwa Ofedwa
KUŴAŴA KWA IMFA
Kodi umoyo umakhala bwanji munthu akafedwa? N’cifukwa ciani anthu ofedwa afunika citonthozo?
ZIMENE MUNGAYEMBEKEZELE
Nkhani iyi, ifotokoza maganizo amene anthu amakhala nawo ponena za cisoni, komanso zimene ambili amacita akafedwa. Ngati munafedwa, dziŵani kuti anthu amalila malilo mosiyana-siyana, ndipo zonsezo n’cibadwa.
ZIMENE MUNGACITE PALIPANO MUKAFEDWA
Kodi mungatsatile njila ziti zimene zingakuthandizeni kupilila cisoni? Nkhani iyi, ipeleka malingalilo acindunji amene athandiza ena, ndipo ni ozikidwa pa nzelu zimene n’zothandiza nthawi zonse.
THANDIZO LODALILIKA KWAMBILI KWA OFEDWA
Onani gwelo la citonthozo limene ambili apeza panthawi yovuta kwambili, komanso onani mmene ingakuthandizileni.