Pa nthawi ya mavuto aakulu, tetezani ubale wanu na anthu amene mumakonda mwa kucita izi
LIMBITSANI UKWATI WANU
Kulimbitsa ukwati wanu
Baibo imati: “Aŵili amaposa mmodzi . . . Ngati mmodzi wa iwo atagwa, winayo akhoza kum’dzutsa mnzakeyo.” (Mlaliki 4:9, 10) Anthu okwatilana ayenela kukhala ngati woyendetsa ndeke na womuthandiza wake, amene ali na colinga copita ku malo amodzi, osati ngati ndeke ziŵili za nkhondo zimene zifuna kuwombana.
Tsimikizani mtima kuti muzicitabe zinthu mokoma mtima na mnzanu wa mu ukwati ngakhale pamene mwapanikizika na mavuto. Kukhala woleza mtima komanso wololela n’kothandiza kwambili.
Kamodzi pa mlungu, muzikambilanako na mwamuna kapena mkazi wanu za mavuto amene muyenela kuwathetsa. Kumbukilani kuti colinga canu ni kuthana na mavutowo osati kuimba mlandu mnzanuyo.
Muzipatulako nthawi yocitila pamodzi zinthu zimene nonse aŵili mumakonda.
Muzikumbukila zinthu zosangalatsa zimene munacitila pamodzi. Mwacitsanzo, mungapatuleko nthawi yoona zithunzi za pa cikwati canu kapena za pa cocitika cina cosangalatsa.
“Mwamuna na mkazi wake sangagwilizane pa ciliconse, koma izi sizitanthauza kuti sangacitile zinthu pamodzi. Iwo angapangile limodzi cisankho na kuthandizana kuti akwanilitse zimene asankhazo.”—David.
KHALANIBE PA UBALE WABWINO NA ENA
Kulimbitsa ubale wanu na ena
Musamangoganizila mmene mabwenzi anu angakuthandizileni , koma muziganizilanso mmene inuyo mungathandizile ena. Mukamalimbikitsa ena, inunso mumalimbikitsidwa.
Tsiku lililonse, muzikambilanako na anzanu ena kuti mudziwe za umoyo wawo.
Afunseni kuti akuuzeni zimene zimawathandiza kupilila mavuto ofanana na amene inu mukukumana nawo.
“Munthu ukakumana na mavuto aakulu, umakhala ngati uli mumdima. Mabwenzi angakuthandize kudziŵa pamene uli komanso kumene uyenela kuloŵela. Angacite zimenezi mwina mwa kungokukumbutsa zinthu zimene ukuzidziŵa kale. Mabwenzi amakukonda, ndipo amadziŵa kuti nawenso umawakonda.”—Nicole.
MUZILIMBIKITSA ANA ANU
Kulimbikitsa ana anu
Baibo imati: “Munthu aliyense akhale wofulumila kumva, wodekha polankhula.” (Yakobo 1:19) Poyamba, ana anu sangakhale omasuka kufotokoza zimene amaopa kapena kuda nazo nkhawa. Koma mukamawamvetsela moleza mtima, mungawathandize kukhala omasuka.
Muzicitako zinthu zimene zingathandize ana anu kukhala omasuka kukamba za kumtima kwawo. Ana ena sakhala omasuka kulankhula ngati mwacita kukhala nawo pansi kuti mukambilane nawo. Koma amakhala omasuka ngati mucita nawo zinthu zina monga kuyenda pa motoka kapena pansi.
Onetsetsani kuti ana anu samvetsela kapena kuonelela kwambili nkhani zocititsa mantha.
Auzeni ana anu zimene mwakonza kuti muteteze banja lanu.
Konzekelani zoyenela kucita pakagwa tsoka, ndipo yesezani zimenezo pamodzi ndi ana anu.
“Muzikambilana na ana anu, na kuwalola kufotokoza mmene akumvela. Iwo angakhale na mantha, nkhawa, kapena mkwiyo, koma osamasuka kufotokoza. Auzeni kuti inunso mumamva cimodzimodzi nthawi zina, ndipo afotokozeleni zimene zimakuthandizani mukamva conco.”—Bethany.