LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • my nkhani 21
  • Abale Ake Amuzonda Yosefe

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Abale Ake Amuzonda Yosefe
  • Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Nkhani Zofanana
  • ‘Tamvelani Maloto Awa’
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • Kapolo Amene Anamvela Mulungu
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Yehova Sanamuiŵale Yosefe
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Banja Lonse Lisamukila Ku Iguputo
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
Onaninso Zina
Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
my nkhani 21

Nkhani 21

Abale Ake Amuzonda Yosefe

WAONA mnyamata uyu pacithunzi-thunzi aonekela? Ali wacisoni ndi wovutika maganizo kwambili. Dzina lake ni Yosefe. Abale ake amugulitsa kwa anthu awa amene ali paulendo wopita ku Iguputo. Yosefe adzakhala kapolo kumeneko. Nanga n’cifukwa ciani abale ake amenewa anacita cinthu coipa cimeneci? N’cifukwa cakuti anali kumucitila nsanje.

Yosefe anali kukondedwa kwambili ndi Yakobo, atate ake. Anali kumuyanja kwambili, cakuti anamusokela mkanjo wabwino kwambili. Pamene akulu ake 10 anaona mmene Yakobo anali kukondela Yosefe, anayamba kumucitila nsanje ndi kumuzonda. Koma panalinso cifukwa cina cimene anali kumuzondela.

Yosefe analota malota aŵili. Mu maloto onse a Yosefe abale ake anali kumugwadila. Pamene Yosefe anauza abale ake za maloto amenewa, cidani cao cinakulilatu.

Tsiku lina pamene abale a Yosefe anali kulisha nkhosa za atate ao, Yakobo anapempha Yosefe kuti apite kukaona abale ake kumene anali kulishila mbelele. Pamene abale ake anamuona kuti wabwela, ena anati: ‘Tiyeni timuphe!’ Koma Rubeni, wamkulu pa onse, anati: ‘Iyai, musacite zimenezo!’ M’malo mwake, anamugwila Yosefe ndi kumuponya m’citsime copanda madzi. Ndiyeno abale ake anakhala pansi kuganizila cakuti acite naye.

Panthawi imeneyi Aisimaeli anali kuyenda mu njila. Ndiyeno Yuda anauza abale ake kuti: ‘Tiyeni timugulitse kwa Aisimaeli.’ Ndipo ni zimene io acita. Amugulitsa ndalama zasiliva zokwana 20. Iwo anali ouma mtima ndi opanda cifundo.

Kodi abale ake amenewa adzauza ciani atate ao? Iwo akupha mbuzi ndi kuviika mkanjo wake wokongola m’magazi a mbuziyo. Ndiyeno atenga mkanjo ndi kupita nao kwa atate ao a Yakobo, ndipo akuti: ‘Tapeza mkanjo uwu. Uonetsetseni kuti muone ngati ni wa Yosefe kapena iyai.’

Yakobo aona kuti mkanjowo ni wa Yosefe. Iye alila kuti: ‘Cilombo ca kuthengo camupha Yosefe.’ Ndipo izi n’zimene abale a Yosefe afuna kuti atate ao akhulupilile. Yakobo ali ndi cisoni kwambili. Alila kwa masiku ambili. Komabe Yosefe sanafe. Tiye tione zimene zimucitikila kumene iye watengedwa.

Genesis 37:1-35.

Mafunso Ophunzilila

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani