LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w14 9/1 masa. 10-14
  • ‘Tamvelani Maloto Awa’

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • ‘Tamvelani Maloto Awa’
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • MBILI YA BANJA LALIKULU
  • NSANJE IKULA MSINKHU
  • MALOTO A YOSEFE
  • CIDANI CIFIKA PACIMAKE
  • Abale Ake Amuzonda Yosefe
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Kapolo Amene Anamvela Mulungu
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Yehova Sanamuiŵale Yosefe
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Banja Lonse Lisamukila Ku Iguputo
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
w14 9/1 masa. 10-14

TENGELANI CITSANZO CAO | YOSEFE

‘Tamvelani Maloto Awa’

YOSEFE anayang’ana kum’mawa ndi mtima wacisoni, kulakalaka kuthawa amalonda amene anali nao. Iye anadziŵa kuti kuseli kwa mapili aja ku Heburoni n’kumene kunali nyumba ya makolo ake. A Yakobo, atate ake, sanadziŵe ciliconse cimene cacitikila mwana wao wapamtima, ndipo adzakhala akumuyembekezela madzulo. Yosefe wacinyamatayo anadziŵa kuti palibe ciliconse cimene angacite ndipo sadzaonananso ndi atate ake okalamba. Amalondawo anali kumuyang’anila pamene anali kuuza ngamila zao kulowela njila ya kum’mwela. Yosefe anali wao tsopano ndipo sanasiye kumuyang’anila. Iwo anaona mnyamata ameneyo ngati katundu wamtengo wapatali kwambili, cakuti anaona kuti akapita naye ku Iguputo adzawapezetsa phindu kwambili.

Yosefe anali ndi zaka 17. Yelekezani kuti mukuona Yosefe akuyang’ana kuthambo lakumadzulo kumene dzuŵa linali pafupi kuloŵa, ndipo akuganizila mmene zinthu zafikila poipa kwambili pa umoyo wake. Yosefe sanakhulupilile kuti abale ake enieni anatsala pang’ono kumupha ndipo anamugulitsa kuti akakhale kapolo. Yosefe analila cifukwa ca zimenezi. Iye sanadziŵe n’komwe mmene tsogolo lake lidzakhalila.

Kodi Yosefe anapezeka bwanji mu vuto limeneli? Nanga tingaphunzilepo ciani pa cikhulupililo ca mnyamata amene ananzunzidwa ndi kukanidwa ndi anthu a m’banja lake?

MBILI YA BANJA LALIKULU

Yosefe anali kucokela ku banja lalikulu, limene linali losagwilizano ndi losasangalala. Citsanzo ca m’Baibulo ca banja la Yakobo cikuonetsa kuipa kwa kukwatila mitala. Panthawi imeneyo, Mulungu anavomeleza mwambo umenewu pakati pa anthu ake. Koma Yesu atabwela anaika lamulo lakuti anthu asakwatile mitala. (Mateyu 19:4-6) Yakobo anali ndi ana 14 amene sanali a mimba imodzi. Iye anali ndi akazi 4, akazi ake enieni anali Leya ndi Rakele ndipo adzakazi ao anali Zelipa ndi Biliha. Yakobo kuyambila paciyambi anakonda kwambili Rakele amene anali wokongola. Iye sanali kukonda mkulu wake Leya amene atate ao anapeleka kwa Yakobo kukhala ngati ndi Rakele amene Yakobo anali kufuna kukwatila poyamba. Ndiyeno akazi aŵiliwa anayamba kulimbana kwambili ndipo nsanje imeneyo inayambukila ana onse pa nyumbapo.—Genesis 29:16-35; 30:1, 8, 19, 20; 37:35.

Rakele sanali kubeleka kwa nthawi yaitali, koma pomaliza pake anabala Yosefe amene Yakobo anamuona kuti anali mwana wapadela kwambili popeza anali atabadwa iye atakalamba. Mwacitsanzo, pamene banja la Yakobo linali paulendo woosa wokakumana ndi Esau mbale wake amene anali kufuna kumupha pa nthawi ina, iye anatsimikiza kuti Rakele ndi Yosefe wacicepele aikidwa pamalo abwino kwa gulu lonse la a m’nyumba yake. Tsiku limeneli liyenela kuti linali losaiwalika kwa Yosefe. Iye ayenela kuti anadabwa kwambili m’mawa mmenemo kuona atate ake amene anali wokalamba koma amphamvu akuyenda cotsimphina. Iye anadabwa atadziŵa cifukwa cake: Atate wake analimbana ndi mngelo wamphamvu usiku wonse! Cifukwa ciani? Cifukwa Yakobo anali kufuna madalitso ocokela kwa Yehova Mulungu. Dalitso limene Yakobo analandila linali kusintha dzina lake kukhala Isiraeli. Mtundu wonse unali kudzachedwa ndi dzina lake! (Genesis 32:22-31) Patapita nthawi, Yosefe anadziŵa kuti ana a Isiraeli adzakhala tate wa mafuko a mtunduwo!

Patangopita nthawi zinthu zomvetsa cisoni zinamucitikila Yosefe, munthu amene anali kukonda kwambili anamusiya. Ameneyo anali amai ake amene anamwalila pamene anali kubeleka Benjamini mng’ono wake. Atate wake anamva cisoni kwambili ndi imfa imeneyi. Yelekezani kuti mukuona Yakobo atate ake a Yosefe akumupukuta misozi mokoma mtima, kenako akumutonthoza pomulimbikitsa kukhala ndi ciyembekezo cimene cinatonthoza agogo ake a Abulahamu. Yosefe ayenela kuti anakhudzidwa ndi kulimbikitsidwa kwambili kudziŵa kuti nthawi ina Yehova adzaukitsa amai ake kwa akufa. N’kutheka kuti mwina zimenezi zinacititsa Yosefe kukonda kwambili “Mulungu . . . wa anthu a moyo” amene ndi wopatsa. (Luka 20:38; Aheberi 11:17-19) Mkazi wake atamwalila, Yakobo anali kukonda kwambili ana ake aamuna aŵili amene Rakele anamubelekela.—Genesis 35:18-20; 37:3; 44:27-29.

Ana ambili amakhala opusa kapena kukhala osamvela ngati makolo ao amawacitila zilizonse zimene akufuna; koma si mmene Yosefe analili, iye anaphunzila makhalidwe abwino ambili kwa makolo ake ndipo anali wolimba m’cikhulupililo ndiponso anali kusiyanitsa cabwino ndi coipa. Pamene Yosefe anali ndi zaka 17, tsiku liina anapita kukathandiza abale ake kugwila nchito yaubusa ndipo anaona zoipa zimene io anali kucita. Kodi iye anaganizako zakuti asaulule zoipa zimenezo ndi colinga cakuti abale akewo amukonde? Ai, iye anasankha kucita zinthu zoyenela. Iye anakauza atate wake za nkhaniyo. (Genesis 37:2) Mwinamwake kulimba mtima kumeneko kunacititsa Yakobo kukhala ndi maganizo oyenela kulinga kwa mwana wake wokondedwa. Cimeneci ndi citsanzo cabwino kwambili cofunika kuciganizila makamaka Akristu acinyamata. Pamene mukuyesedwa kuti mubise chimo lalikulu, kaya la mng’ono wanu kapena la mnzanu, mungacite bwino kutengela citsanzo ca Yosefe ndi kutsimikiza kuti mwaulula nkhaniyo kwa amene angafunike kuisamalila ndi kuthandiza wolakwayo.—Levitiko 5:1.

Tingatengenso phunzilo lina ku banja limene Yosefe anali kucokela. N’zoona kuti masiku ano, Akristu sangakwatile mitala, koma pakati pao pamapezeka mabanja ogaŵanika, makolo opeza, ana opeza ndi ang’ono kapena akulu athu opeza. Pa citsanzo ca banja la Yakobo, tikuphunzilapo kuti kukhala ndi mtima wokondela ndi watsankho m’banja kumasokoneza mgwilizano wa banja. Makolo anzelu amene ali ndi mabanja ogaŵanika, amacita zilizonse zimene angathe kuti akondweletse ana ao ndi ana opeza kuti aliyense azidzimva kuti ndi wokondedwa ndipo anadalitsidwa ndi mphatso yapadela ndi kuti aliyense akusangalala m’banja.—Aroma 2:11.

NSANJE IKULA MSINKHU

Kulimba mtima kwa Yosefe pofuna kucita cilungamo, kunacititsa Yakobo atate ake kumupatsa mphatso yaulemu. Iye anasoketsela mwana wake ameneyo covala cabwino kwambili. (Genesis 37:3) Covala cimeneco cimachedwa mkanjo wamizelemizele kapena kuti wamaŵangamaŵanga. Ngakhale kuti sizikudziŵika bwinobwino mmene mkanjowo unalili. Zioneka kuti mkanjowo unali wautali, wokongola, wa manja aatali. Covala cimeneco cinali kuvalidwa ndi anthu olemekezeka kapena mafumu.

Zimene Yakobo anacita zinali ndi tanthauzo labwino kwambili ndipo Yosefe anakhudzidwa kwambili ndi cikondi cimene bambo ake anamuonetsa. Koma pambuyo pake, covala cimeneco cinamubweletsela mavuto. Kumbukilani kuti mnyamatayo anali kugwila nchito ya ubusa. Kutanthauza kuti inali nchito yovuta kwambili. Yelekezelani kuti mukuona mnyamatayu atavala covala cacifumu, akupita m’maudzu aatali, akukwela m’phili ndipo akupita m’chile mmene muli minga kufunafuna nkhosa yotayika. Kuonjezela apo, zikhala bwanji abale ake akaona mphatso imene atate ao amupatsa?

Baibulo limayankha kuti: “Abale ake ataona kuti bambo ao anali kukonda kwambili Yosefe kuposa io onse, anayamba kudana naye cakuti sanali kulankhula naye mwamtendele.”a (Genesis 37:4) Nsanje yao inali yomveka, koma kunali kupanda nzelu kulola kutengeka ndi nsanje yoipa imeneyo. (Miyambo 14:30; 27:4) Kodi munacitapo nsanje mutaona kuti winawake waonetsedwa cikondi kapena kupatsidwa ulemu umene inu munali kuuyembekezela? Kumbukilani citsanzo ca abale ake a Yosefe. Nsanje yao inawasonkhezela kucita zinthu zimene patsogolo pake anadzacita nazo cisoni. Citsanzo cao cimakumbutsa Mkristu aliyense kuti cimakhala cinthu canzelu “kusangalala ndi amene akusangalala.”—Aroma 12:15.

Yosefe anazindikila kuti abale ake amamuzonda kwambili. Cotelo, kodi iye anabisa mkanjo wapadela umene anapatsidwa ndi atate ake, abale ake atamuyandikila? Ayenela kuti anali ataganizapo kutelo. Koma kumbukilani kuti Yakobo anafuna kuti mkanjowo ukhale cizindikilo ca kukoma mtima ndi cikondi. Popeza kuti Yosefe anali kufuna kuti bambo ake apitilize kumudalila, iye anapitilizabe kuvala mkanjo umene anamupatsa. Citsanzo cake ndi cofunika kwambili kwa ife. Ngakhale kuti Atate wathu wa kumwamba alibe tsankho, nthawi zina iye amasankha atumiki ake okhulupilika ndi kuwakomela mtima. Kuonjezela apo, iye amawapempha kukhala osiyana ndi dzikoli limene ladzaza ndi makhalidwe oipa. Mofanana ndi mmene mkanjo wapadela wa Yosefe unalili, khalidwe la Akristu oona, liyenela kukhala losiyana ndi la anthu owazungulila. Kukhala ndi khalidwe limeneli kumacititsa anthu ena kuti aziticitila nsanje ndi kutida. (1 Petulo 4:4) Kodi Mkristu ayenela kubisa kuti ndi mtumiki wa Mulungu? Iyai—Yosefe sanabise mkanjo wake.—Luka 11:33.

MALOTO A YOSEFE

Pasanapite nthawi yaitali Yosefe analota maloto aŵili odabwitsa. Maloto oyambilila analota kuti, iye ndi abale ake akumanga mitolo ya tiligu. Koma pamene mtolo wake unadzuka n’kuima cilili, mitolo ya abale ake inadzuka ndipo inazungulila mtolo wake n’kuyamba kuuŵelamila. Mu maloto aciŵili analota kuti, dzuŵa, mwezi ndiponso nyenyezi zokwanila 11 zikumugwadila. (Genesis 37:6, 7, 9) Popeza kuti malotowo anali acilendo ndi osaiwalika, kodi Yosefe akanacita ciani?

Maloto amenewo anali ocokela kwa Yehova Mulungu. Malotowo anali maulosi ndipo Mulungu anafuna kuti Yosefe apeleke uthenga umene unali mu maloto amenewo. Tinganene kuti Yosefe anali kufunika kucita zinthu monga mmene aneneli amene anadzakhalapo ndi moyo anali kucitila pofotokoza mauthenga a Mulungu ndi ziweluzo Zake kwa anthu ake osamvela.

Mocenjela Yosefe anati kwa abale ake: “Mvelani maloto amene ine ndinalota.” Abale ake anamvetsela maloto amenewo koma sanakondwele nao ngakhale pang’ono. Ndiyeno iwo anamuyankha kuti: “Kodi iweyo ndithu ukuganiza kuti ungadzakhale mfumu yathu?” Nkhaniyo imapitiliza kuti: “Kwa io maloto amenewo ndi mau akewo cinakhala cifukwa cinanso comudela.” Yosefe atafotokoza loto laciŵili kwa atate ake ndiponso kwa abale ake, iwo sanayankhe bwino. Timaŵelenga kuti: “Bambo ake anamudzudzula kuti: ‘Kodi maloto walotawa akutanthauza ciani? Kodi ineyo ndithu ndi mai akowa, komanso abale akowa tidzagwada pansi pamaso pa iwe?’” Komabe Yakobo anapitiliza kuganizilapo pa mau a Yosefe. Moti iye anadzifunsa kuti, kodi mnyamata ameneyu angakhale kuti amalankhula ndi Yehova?—Genesis 37:6, 8, 10, 11.

Yosefe sanali mtumiki woyamba kapena womaliza wa Yehova kuuzidwa kuti apeleke uthenga wa ulosi umene sudzasangalatsa anthu ndipo udzamubweletsela cizunzo. Yesu anali wopeleka uthenga wamkulu kuposa anthu amene anacitila umboni uthenga wotelo, cakuti anauza otsatila ake kuti: “Ngati anazunza ine, inunso adzakuzunzani.” (Yohane 15:20) Akristu a misinkhu yonse angaphunzile zambili pa cikhulupililo ndi kulimba mtima kwa Yosefe wacinyamata.

CIDANI CIFIKA PACIMAKE

Posakhalitsa, Yakobo anatumiza mnyamata Yosefe paulendo. Ana ake akuluakulu anapita kukadyetsela ziŵeto kufupi ndi Sekemu kumene anakumana ndi adani pasanapite nthawi. Yakobo mwacibadwa anali kudela nkhaŵa ana ake ndiye cifukwa cake anatumiza Yosefe kuti akaŵaone mmene alili. Kodi muganiza kuti Yosefe anamva bwanji? Iye anali kudziŵa kuti abale ake amamuda kothelatu. Ndiyeno bwanji akaona kuti iye akulankhulila atate ao. Mosasamala kanthu za zimenezi, Yosefe anamvela bambo ake ndipo anapita.—Genesis 34:25-30; 37:12-14.

Unali ulendo wautali ndithu mwina wa masiku 4 kapena 5 kuyenda pansi. Pali mtunda wa makilomita pafupifupi 80 kucoka ku mphoto kwa Heburoni kufika ku Sekemu. Koma ali ku Sekemu, Yosefe anadziŵa kuti abale ake apita ku Dotana komwe kunali mtunda wa makilomita 22 kuloŵela kumphoto. Pamene Yosefe anafika ku Dotana, abale ake anamuonela patali. Atangomuona mitima yao inawila moti mkwiyo wao unayaka. Nkhaniyo imati: “Cotelo iwo anauzana kuti: ‘Tamuonani wolota uja. Uyo akubwela apoyo. Motelo io anati tiyeni timuphe timuponye m’citsime copanda madzi ndipo tikanene kuti cilombo colusa camudya. Ndiyeno tidzaone cidzacitike ndi ciani ku maloto ake aja.’” Koma Rubeni anapempha abale akewo kuti asamuphe Yosefe m’malo mwake amuponyele m’citsime copanda madzi ali wa moyo ndi colinga cakuti iye amupulumutse nthawi ina.—Genesis 37:19-22.

Mosazindikila kuti io apangana zotani, Yosefe anafika ndi maganizo akuti zonse zili bwino. M’malo mwake abale akewo anamucita zacipongwe. Anamuvula mwankhanza mkanjo wake wapadela, anamuguzila ku citsime ca matope ndi kumukankhilamo. Kenako Yosefe anagwelamo. Ali wosokonezeka maganizo, Yosefe anayesayesa kuona mmene angatulukile koma analephela. Iye anali kumva mau a abale ake akuzimililika pang’onopang’ono ali m’citsime ndipo anali kuona cabe kathambo kozungulila. Anawalilila ndi kuwacondelela koma io anamunyalanyaza. Iwo mouma mtima, anadya cakudya pafupi ndi citsimeco. Pamene Rubeni anacokapo, abale akeo anaganizanso zomupha mnyamatayo, koma Yuda anapempha kuti amugulitse ku gulu la apaulendo m’malo momupha. Ku Dotana kunali kufupi ndi njila ya malonda yopita ku Iguputo, ndipo pasanapite nthawi gulu la apaulendo la Aisimayeli ndi Amidiyani linabwela. Rubeni asanafikebe io anacita zimene anapangana. Iwo anagulitsa mbale wao ndi ndalama 20 zasiliva kuti akakhale kapolo.b—Genesis 37:23-28; 42:21.

Ndiyeno tibwelelenso ku mfundo yoyamba ija. Pamene Yosefe anatengedwa kuloŵela kum’mwela njila yopita ku Iguputo, anaoneka ngati watayika. Iye mokakamizika anapatulidwa. Sanadziŵe ciliconse cokhudzana ndi banja lake kwa zaka zambili—sanadziŵe zimene Rubeni anacita atapeza kuti Yosefe kulibe; sanadziŵe cisoni cimene Yakobo anamva atanamizidwa kuti akhulupilile bodza lakuti mwana wao wokondedwa Yosefe anamwalila; sanadziŵe mmene analili agogo ake a Isaki amene anali atakalamba kwambili; ndiponso sanadziŵe za Benjamini mng’ono wake wokondedwa, amene anali kumuyewa kwambili. Koma pali cina cimene Yosefe anali naco.—Genesis 37:29-35.

Cinthu cimene abale ake a Yosefe analephela kumulanda cinali cikhulupililo. Iye anali kudziŵa zambili ponena za Yehova Mulungu wake, ndipo palibe amene akanatha kumulanda zimenezo, kaya kutayikilidwa banja lake, kaya zovuta za paulendo wautali wopita ku Iguputo, ngakhale kucita manyazi pogulitsidwa kwa munthu wacuma wa ku Iguputo dzina lake Potifala. (Genesis 37:36) Zovuta zonse zimene Yosefe anakumana nazo zinacititsa kuti cikhulupililo ca Yosefe cikule ndi kuti ayandikane kwambili ndi Mulungu. Mu nkhani za mtsogolomu, tidzaona mmene cikhulupililo ca Yosefe cinamucititsila kukhala wofunika kwa Mulungu wake Yehova ndi kwa banja lake lovutalo. Kutengela citsanzo ca Yosefe cingakhale cinthu canzelu kwambili

a Ofufuza ena anafotokoza kuti abale ake a Yosefe anaona kuti mphatso imene bambo wao anapatsa Yosefe inapeleka umboni wonena kuti iye anali kufuna kuti mnyamatayo alandile ufulu wa mwana woyamba kubadwa. Iwo anadziŵa kuti Yosefe anali mwana woyamba kubadwa kwa mkazi wake wokondedwa—amene anafunika kukwatila paciyambi. Patapita nthawi, Rubeni mwana woyamba wa Yakobo anagona ndi Biliha mkazi wacinai wa atate ake, ndiyeno anacititsa manyazi atate ake ndipo mwacionekele anataya mwai wokhala mwana woyamba kubadwa kapena wamkulu.—Genesis 35:22; 49:3, 4.

b Ngakhale ndi mau ocepa amenewa, Baibulo limaonetsa kuti zimenezi n’zoona. Nkhani zolembedwa za m’nthawi imeneyo zionetsa kuti munthu anali kugulitsidwa ndi kupita ku ukapolo ku Iguputo ndi masekeli 20.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani