PHUNZILO 6
Kodi Tili ndi Ciyembekezo Canji Ponena za Akufa?
1. Kodi uthenga wabwino pankhani ya akufa ni wakuti bwanji?
Yesu atafika ku Betaniya pafupi ndi Yerusalemu, panali patapita masiku anai kucokela pamene bwenzi lake Lazaro anamwalila. Yesu anapita kumanda a Lazaro pamodzi ndi Malita ndi Mariya, alongosi a womwalilayo. Posapita nthawi, anthu anasonkhana. Malita ndi Mariya anasangalala kwambili pamene Yesu anaukitsa Lazaro.—Ŵelengani Yohane 11:21-24, 38-44.
Malita anali kudziŵa kale zimene uthenga wabwino unanena za akufa. Iye anali kudziŵa kuti Yehova adzaukitsa akufa kuti adzakhalenso ndi moyo padziko lapansi.—Ŵelengani Yobu 14:14, 15.
2. Kodi akufa ali mu mkhalidwe wabwanji?
Mulungu anauza Adamu kuti: “Popeza ndiwe fumbi, kufumbiko udzabwelela.”—GENESIS 3:19.
Anthu anapangidwa ndi dothi. (Genesis 2:7; 3:19) Sindife mizimu imene ili m’thupi lanyama. Koma ndife zolengedwa zokhala ndi thupi lanyama, ndipo tikamwalila palibe ciliconse cimene cimapitiliza kukhala ndi moyo. Tikafa, ubongo wathu naonso umafa, ndipo timaleka kuganiza. N’cifukwa cake pamene Lazaro anaukitsidwa sanakambe ciliconse cokhudza mkhalidwe wa akufa cifukwa io sadziŵa ciliconse.—Ŵelengani Salimo 146:4; Mlaliki 9:5, 6, 10.
Kodi Mulungu amazunza anthu m’moto akamwalila? Popeza kuti Baibo imaonetsa kuti akufa sadziŵa ciliconse, n’zoonekelatu kuti ciphunzitso ca moto wa kuhelo n’cabodza. Cimaipitsa dzina la Mulungu. Mulungu sangaganize zozunza anthu m’moto cifukwa cakuti maganizo amenewo ni oipa kwambili.—Ŵelengani Yeremiya 7:31.
Tambani vidiyo Kodi Akufa Ali mu Mkhalidwe Wabwanji?
3. Kodi akufa angakambe ndi ife?
Akufa sangakambe kapena kumva. (Salimo 115:17) Koma pali angelo oipa, amene amatha kukamba kwa anthu ndi kuyelekezela kuti ndi anthu amene anamwalila. (2 Petulo 2:4) Yehova amatiletsa kufunsila kwa akufa.—Ŵelengani Deuteronomo 18:10, 11.
4. Kodi ndani adzaukitsidwa?
Anthu akufa mamiliyoni ambili amene ali m’manda adzakhalanso ndi moyo padziko lapansi. Ngakhale ena amene sanadziŵe Mulungu ndipo anali kucita zoipa adzaukitsidwa.—Ŵelengani Luka 23:43; Machitidwe 24:15.
Anthu amene adzaukitsidwa adzaphunzila coonadi ca Mulungu ndi kuonetsa cikhulupililo mwa Yesu mwa kumumvela. (Chivumbulutso 20:11-13) Anthu amene adzakhalanso ndi moyo ndi kucita zinthu zabwino adzakhala ndi moyo wamuyaya padziko lapansi.—Ŵelengani Yohane 5:28, 29.
5. Kodi ciukililo cimatiuza ciani za Yehova
Ciyembekezo cakuti akufa adzauka cidzakwanilitsidwa cifukwa cakuti Mulungu anatumiza Mwana wake kuti adzatifele. Mwa ici, ciukililo cimatiuza za cikondi ca Yehova ndi cisomo cake. Pamene akufa adzauka, ndani maka-maka amene mudzafuna kuona?—Ŵelengani Yohane 3:16; Aroma 6:23.