KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBO
Kodi akufa adzakhalanso ndi moyo?
Imfa ili ngati tulo cifukwa cakuti munthu wakufa palibe cimene amadziŵa ndipo sangacite ciliconse. Koma Mlengi wa moyo angathe kuukitsa akufa. Mulungu anaonetsa kuti angathe kucita zimenezi mwa kupatsa Yesu mphamvu kuti aukitse anthu angapo akufa.—Ŵelengani Mlaliki 9:5; Yohane 11:11, 43, 44.
Mulungu walonjeza kuti adzaukitsa anthu amene akuwakumbukila kuti adzakhale ndi moyo padziko lapansi latsopano. Anthu akufa ali kumanda kuyembekezela nthawi imene Mulungu adzawaukitsa. Mulungu Wamphamvuyonse amalaka-laka kuukitsa anthu amene anafa.—Ŵelengani Yobu 14:14, 15.
Kodi ciukililo cidzacitika bwanji?
Anthu amene Mulungu adzaukitsa adzakwanitsa kudzidziŵa io eni. Adzakwanitsanso kudziŵa mabwenzi ao ndi acibanja ao. Ngakhale kuti anthu akafa matupi ao amaola, Mulungu sangalephele kuukitsa anthu amenewo ndi matupi atsopono.—Ŵelengani 1 Akorinto 15:35, 38.
Anthu ocepa amaukitsidwa ndi kupita kumwamba. (Chivumbulutso 20:6) Anthu ambili amene adzaukitsidwa adzakhala ndi moyo padziko lapansi la paladaiso. Iwo adzakhala ndi umoyo watsopano ndiponso mwai wokhala ndi moyo wamuyaya.—Ŵelengani Salimo 37:29; Machitidwe 24:15.
Kuti mudziŵe zambili, onani nkhani 6 ndi 7 m’buku ili, Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova
Mungatenge buku limeneli pa www.jw.org
[Cithunzi papeji 32]
Kodi imfa imafanana bwanji ndi tulo?