LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • T-35 masa. 1-4
  • Kodi N’zoona Kuti Akufa Angakhalenso ndi Moyo?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi N’zoona Kuti Akufa Angakhalenso ndi Moyo?
  • Kodi N’zoona Kuti Akufa Angakhalenso ndi Moyo?
  • Nkhani Zofanana
  • Kodi Zinthu Zidzakhala Bwanji Mtsogolo?
    Kodi Zinthu Zidzakhala Bwanji Mtsogolo?
  • Kodi Mavuto Adzathadi?
    Kodi Mavuto Adzathadi?
  • Kodi Ndani Maka-maka Amene Akulamulila Dzikoli?
    Kodi Ndani Maka-maka Amene Akulamulila Dzikoli
  • Kodi Ufumu wa Mulungu Ndi Ciani?
    Kodi Ufumu wa Mulungu Ndi Ciani?
Onaninso Zina
Kodi N’zoona Kuti Akufa Angakhalenso ndi Moyo?
T-35 masa. 1-4
Makolo ayang’ana zithunzi-thunzi za mwana wao wamng’ono amene wamwalila

Kodi N’zoona Kuti Akufa Angakhalenso ndi Moyo?

Kodi mungayankhe kuti . . .

  • inde?

  • iyai?

  • kapena?

ZIMENE BAIBO IMANENA

“Kudzakhala kuuka.”—Machitidwe 24:15, Baibulo la Dziko Latsopano.

MAPINDU OKHULUPILILA KUTI AKUFA ADZAUKA

Kukhulupilila zimenezi kudzakutonthozani munthu amene mumakonda akamwalila.—2 Akorinto 1:3, 4.

Simudzaopa imfa mopambanitsa.—Aheberi 2:15.

Mudzakhala ndi ciyembekezo ceni-ceni cakuti mudzaonanso okondedwa anu amene anamwalila.—Yohane 5:28, 29.

Banja ndi mkazi wa masiye alimbikitsidwa ndi nkhani ya ciukililo

KODI TINGAKHULUPILILEDI ZIMENE BAIBO IMANENA?

Inde, pa zifukwa zitatu izi:

  • Mulungu ndiye Mlengi wa moyo. Baibo imacha Yehova Mulungu kuti ndi “kasupe wa moyo.” (Salimo 36:9; Machitidwe 17:24, 25) Iye amene anapatsa moyo colengedwa ciliconse, sangalephele kubwezeletsa moyo wa munthu amene wamwalila.

  • Mulungu anaukitsapo anthu m’nthawi zakale. Baibo imafotokoza za anthu 8 amene anaukitsidwa padziko lapansi. Anthu amenewo anali ana, akulu, amuna ndi akazi. Ena anali akufa kwa nthawi yocepa, koma mmodzi anali m’manda kwa masiku anai.—Yohane 11:39-44.

  • Mulungu ndi wofunitsitsa kuukitsanso akufa. Yehova amadana ndi imfa, ndipo amaiona kuti ndi mdani. (1 Akorinto 15:26) Iye ‘amalaka-laka’ kugonjetsa mdani ameneyo. Iye adzacotsapo imfa mwa kuukitsa akufa. Mulungu amafunitsitsa kuukitsa anthu amene ali m’cikumbukilo cake kuti adzakhalenso ndi moyo padziko lapansi.—Yobu 14:14, 15.

GANIZILANI FUNSO ILI

Kamnyamata kakula ndi kukalamba

N’cifukwa ciani timakalamba ndi kufa?

Baibo imayankha funso limenelo pa GENESIS 3:17-19 ndi pa AROMA 5:12.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani