LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • yc phunzilo 11 masa. 24-25
  • Analemba za Yesu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Analemba za Yesu
  • Phunzitsani Ana Anu
  • Nkhani Zofanana
  • Kodi Yesu Khiristu N’ndani?
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
  • Limbikilani Monga Anacitila Petulo
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
Phunzitsani Ana Anu
yc phunzilo 11 masa. 24-25
Amuna amene analemba za Yesu anali Mateyu, Maliko, Luka, Yohane, Petulo, Yakobo, Yuda, ndi Paulo

PHUNZILO 11

Analemba za Yesu

Kodi waona amuna amene ali pa cithunzi-thunzi?— Maina ao ndi Mateyu, Maliko, Luka, Yohane, Petulo, Yakobo, Yuda ndi Paulo. Amuna amenewa anakhalapo ndi moyo panthawi imene Yesu anali ndi moyo, ndipo analemba za Yesu. Tiye tiphunzile zambili ponena za io.

Kodi udziŵako ciani za amuna awa?

Atatu anali atumwi amene anali kulalikila ndi Yesu. Kodi uwadziŵa amuna atatu amenewa?— Anali Mateyu, Yohane ndi Petulo. Mtumwi Mateyu ndi mtumwi Yohane anali kumudziŵa kwambili Yesu cakuti onse aŵili analemba mabuku onena za iye. Mtumwi Yohane analembanso buku lochedwa Chivumbulutso, ndi makalata atatu ochedwa Yohane Woyamba, Yohane Waciŵili ndi Yohane Wacitatu. Mtumwi Petulo analemba makalata aŵili amene timapeza m’Baibulo. Amachedwa Petulo Woyamba ndi Petulo Waciŵili. M’kalata yake yaciŵili, Petulo analemba za nthawi pamene Yehova analankhula ali kumwamba ponena za Yesu kuti: ‘Uyu ndi mwana wanga amene ndikonda, ndipo ndimakondwela naye.’

Amuna ena amene ali pa cithunzi-thunzi naonso amatiphunzitsa za Yesu m’mabuku amene io analemba. Mmodzi wa io ndi Maliko. Iye ayenela kuti analipo pamene Yesu anali kumangidwa, ndipo anaona zonse zimene zinali kucitika. Wina ndi Luka. Iye anali dokotala ndipo mwina anakhala Mkristu pambuyo pa imfa ya Yesu.

Enanso aŵili olemba Baibulo amene uona pa cithunzi-thunzi anali abale a Yesu. Kodi uwadziŵa maina ao?— Anali Yakobo ndi Yuda. Poyamba io sanali kukhulupilila Yesu, ndipo anali kuganiza kuti anacita misala pang’ono kapena kuti kufuntha. Koma pambuyo pake anakhulupilila Yesu ndi kukhala Akristu.

Munthu wolemba Baibulo womaliza amene uona pa cithunzi-thunzi apa ndi Paulo. Asanakhale Mkristu, anali Saulo. Iye sanali kukonda Akristu ndipo anali kuwacitila nkhanza kwambili. Kodi udziŵa cimene cinapangitsa Paulo kukhala Mkristu?— Tsiku lina ali paulendo, mwadzidzidzi Paulo anamva munthu wina akukamba naye kucoka kumwamba. Anali Yesu. Iye anafunsa Paulo kuti: ‘N’cifukwa ciani ukuwacitila nkhanza anthu amene amandikhulupilila?’ Pambuyo pake, Paulo anasintha ndi kukhala Mkristu. Iye analemba mabuku 14 a m’Baibulo, kuyambila ndi buku la Aroma mpaka Aheberi.

Timaŵelenga Baibulo tsiku lililonse, kodi si conco?— Mwa kuŵelenga Baibulo timaphunzila zinthu zambili zonena za Yesu. Kodi ufuna kudziŵa zambili ponena za Yesu?—

ŴELENGA M’BAIBULO LAKO

  • 2 Petulo 1:16-18

  • Maliko 3:21; 14:51

  • Yuda 1

  • Machitidwe 9:1-18

MAFUNSO:

  • Kodi ndi atumwi ati a Yesu amene analemba za iye?

  • Kodi ndi olemba Baibulo aŵili ati amene anali abale a Yesu?

  • Kodi Paulo anakhala bwanji Mkristu?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani